Kukwaniritsa konse kwa Khristu.



Gawo 1 — Ntchito ya Khristu monga Malo Wokhawo Wopumulira kwa Wotsutsika

Gawo 2 — Kumasulidwa Kwathunthu Kuchoka ku Mphamvu ya Tchimo

Gawo 3 — Ntchito ya Khristu Yogwirika kwa Ife

Gawo 4 — Khristu monga Chida cha Mtima

Gawo 5 — Mau a Khristu monga Mlozo Wokwanira kwathunthu Panjira Yathu

Pamene moyo watengedwa kukaonetsedwa choonadi chake chenicheni cha momwe moyowo ulili pamaso pa Mulungu, kuzama kwa kuonongeka kwake, kutsutsika kwake, komanso kukhumudwa kwake, komanso kuperewera kwathunthu ndi kopanda chiyembekezo, palibe mpumulo ulionse kufikira Mzimu Woyera akavumbulutsira ku mtima Khristu wathunthu ndi wokwaniritsa zonse.

Yankho lokhalo lopezeka ku kuonongeka kwathu ndilo thandizo langwiro la Mulungu.



Thandizo limeneli ndi losavuta, koma ndilo choonadi chofunika kwambiri; ndipo tingathe kunena, ndi chitsimikizo chonse, zimakhala bwino pamene muwerengi aphunzira zimenezi pa iye yekha.

Chinsinsi chenicheni cha mtendere ndicho kupeza mapeto ake a kutsutsika, kuonongeka, kukhala kakasi, kudziyesa wopanda pake; ndiponso pomwepo kupeza Khristu wokwaniritsa zonse monga chipereko cha Mulungu pa zosowa zathu.

Umenewu ndiwo mpumulo weniweni – mpumulo umene sungasokonezedwe.

Pakhoza kukhala chisoni, kutanganidwa, kulimbana, kuyesedwa kwa moyo, kulemedwa kudzera mu mayesero ochuluka, moyo wapendapenda, mayesero ndi zovuta zosiyanasiyana; koma timamva kulimbikitsidwa kuti pamene moyo wabweretsedwadi mwa Mzimu wa Mulungu kukaona mapeto ake, ndi kupuma mwa Khristu wathunthu, moyowo umapeza mtendere umene sungasokonezedwe.

Moyo wosakhazikika wa anthu ochuluka okondedwa a Mulungu ndi zotsatira za kusalandira Khristu wathunthu m’moyo mwawo, monga woperekedwa wa Mulungu kwa iwo.

Nzosakaikitsa kuti zotsatira zomvetsa chisoni ndi zowawa zimenezi zingathe kubwera ndi zotsatira zake zosiyanasiyana, monga malingaliro a chilamulo, nthenda ya chikumbumtima, mtima wodzikundikira, chiphunzitso choipa, mayendedwe a chinsinsi kutsata za dziko lino lapansi, tinthu tina ting’onoting’ono ta mumtima, monga mwa kutsutsana ndi Mulungu, Khristu, komanso umuyaya.

Komabe, chinthu chimene chimayambitsa, timakhulupilira kuti chidzapezeka, mwanjira ina iliyonse, kuti kusoweka kwa mtendere wokhazikika, zimene zili zochitikachitika pakati pa anthu a Ambuye, zimakhala zotsatira za kusaona, kusakhulupilira, zimene Mulungu wakonza kuti Khristu Wake akhale kwa iwo, komanso mwa iwo, ndipo zimenezi kwamuyaya:

Tsopano chimene tikulinga, m’bukuli ndi kuonetsera muwerengi kuchokera m’masamba a m’Mau a Mulungu, kuti chuma chiliko kwa iye mwa Khristu chimene akufunikira, kaya ndi kukumana ndi zokhumba za chikumbumtima chake, zokhumba za mtima wake, kapenanso kufunikira kwa njira zake.

Tidzafunafuna, mwa chisomo cha Mulungu kuonetsera kuti ntchito ya Khristu ndiyo malo enieni okhawo opumira chikumbumtima: Umunthu Wake, choonadi chenicheni cha mtima: Mau ake, chitsogozo chenicheni chokhacho cha panjira.*

GAWO 1.

Ndipo poyamba, tiyeni tikhazikike pang’ono pa

NTCHITO YA KHRISTU MONGA MALO OKHAWO OPUMILA CHIKUMBUMTIMA.

Pakuganizira mutu waukulu umenewu, zinthu ziwiri zimakopa chidwi chathu: choyamba, zomwe Khristu anatichitira ife; chachiwiri, zomwe Iye akutichitira ife.

Choyambacho ife tili ndi chiombolo; ndipo chotsatiracho, tili naye wotiyimira mlandu.

Iye anatifera pamtanda.

Iye akukhala m’malo mwathu pa mpando wachifumu.

Mwa imfa yake yopambana ya chiombolo, Iye anakumana ndi zosoweka zathu ngati ochimwa.

Iye anatenga machimo athu, ndipo anawachotsa kwamuyaya.

Iye anatsutsidwa pamodzi ndi machimo athu onse – machimo a onse okhulupilira mudzina lake.

Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.” (Yes. 53) Ndipo, “Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, wolungama m’malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu.” 1 Petro 3:18.



Chimenechi ndi choonadi chachikulu komanso chofunika ku moyo wosautsika – choonadi chimene chimapezeka pa maziko amene Chikhristu chaphumphu chimapezeka.

Nzosatheka kuti moyo woona wotsitsimutsidwa ulionse, chikumbumtima chounikidwa mwa uzimu, zingathe kupeza mtendere wokhazikika kufikira choonadi cha mtengo wapatali chagwiritsidwa mwa chikhulupiliro chochepa.

Ndikuyenera kudziwa, mwa ulamuliro wa umulungu, kuti machimo anga achotsedwa kwamuyaya pamaso pa Mulungu; kuti Iye mwini anawachotsa munjira yakuti akafikire pa zofunikira zonse za mpando wake wa chifumu, komanso machitachita a chikhalidwe chake; kuti Iye anadzilemekeza yekha pakutaya machimo athu, munjira ya pamwamba komanso yodabwitsa kusiyana kuti anakanditumiza ine ku gehena chifukwa cha machimowo.

Inde, Iye mwini wachita ichi.

Imeneyi ndiyo mfundo komanso kulingana, phata la nkhani yonse.

Mulungu anaika machimo athu pa Yesu, ndipo akutiuza choncho mu Mau ake Woyera, cholinga kuti tikadziwe mwa ulamuliro wa umulungu – ulamuliro umene sunganame.



Mulungu anakonzeratu ichi; Mulungu anachita ichi; Mulungu akuchilankhula chimenechi.

Zonse ndi za Mulungu, kuyambira pachiyambi kufika pamapeto, ndipo tikuyenera kupeza mpumulo m’menemu monga mwana wamng’ono.

Kodi ndingathe kudziwa bwanji kuti Yesu anasenza machimo anga mthupi lake pa mtengo paja?

Mwa ulamuliro omwewo umene umandiuza ine ndinali ndi machimo ofunika kuchotsedwa.

Mulungu, mwa chikondi chake chodabwitsa ndi chosafanizidwa, akunditsimikizira ine, wotsutsika wosauka, wochimwa woyenera gehena, kuti Iye anatenga nkhani yonse yokhudza machimo anga, ndi kuwachotsa munjira yakuti abweretse zokolola zochuluka mu ulemelero wa dzina lake lamuyaya, mu dziko lonse lapansi, pamaso pa nzeru yonse yolengedwa.

Chikhulupiliro cha moyo wa zimenezi chikuyenera kumasula chikumbumtima.

Ngati Mulungu anakwanitsidwa yekha zokhudza machimo anga, inenso ndingathe kukwanitsidwa.

Ndikudziwa kuti ndine wochimwa – ndingathe kukhala mfumu ya anthu ochimwa.

Ndikudziwa machimo anga ndi ochuluka mu chiwerengero kuposa tsitsi la m’mutu mwanga; kuti ndi akuda ngati pakati pa usiku – akuda ngati gehena imene.

Ine ndikudziwa kuti onse mwa machimo amenewa, ngakhale lochepa, likuyenera kutenthedwa ndi moto wa ku gehena.

Ine ndimadziwa chifukwa Mau a Mulungu amandiuza – kuti dontho la uchimo silidzalowa malo ake oyera; kotero pamene ine ndikukhudzika, panalibe njira ina, kupatula kusiyanitsidwa kwamuyaya ndi Mulungu.

Zonse izi ndimadziwa, pamwamba pa ulamuliro woonekeratu ndi wosakaikitsa wa mau amenewa amene anakhazikika kwamuyaya kumwamba.

Komatu chinsinsi chodabwitsa cha mtanda! – chinsinsi cha ulemelero wa chikondi chowombola ine chimene ndikuona Mulungu mwini kuchotsa machimo anga onse – muyeso wakuda ndi woopsa – machimo anga onse, monga umo Iye anawadziwira ndi kuwawerengera.

Ine ndikumuona Iye akuika machimo onse pa mutu pa Mlowam’malo wanga wodalitsika, kuchita naye chifukwa cha machimowo.

Ine ndikuona namondwe ndi mafunde a mkwiyo wa kulungama kwa Mulungu – mkwiyo wake kutsutsana ndi machimo anga – mkwiyo wake umene unakanyeketsa moyo wanga ndi thupi langa ku gehena woopsa wamuyaya; ndikuona machimo anga onse akuzungulira munthu amene anaima m’malo mwanga; amene anandiyimira ine pamaso pa Mulungu; amene anasenza zonse zimene zinandiyenera ine: amene Mulungu woyera anachita naye monga umo akanachitira ndi ine.

Ine ndikuona chilungamo chosakondera, chiyero, komanso kulungama kothana ndi machimo anga, komanso kuwachotsa ndi kuthana nawo kwamuyaya.

Palibe limodzi mwa machimowa linaferedwa kuti likhalepobe!

Palibe kupusitsidwa, palibe chinsinsi, kapenanso kunyozana, palibe kusiyana.

Zimenezi sizingachitike, pamene Mulungu anatenga zonse kukhala m’manja mwake.

Ulemelero wake unali pa chiopsezo; chiyero chake chosasokonekera, ulamuliro wake wamuyaya, kukwezedwa kwa ulamuliro wa boma lake.

Zimenezi zinayenera kuperekedwa mwa nzeru yotere kuti akadzilemekeze yekha pamaso pa angelo, anthu ndi ziwanda.

Iye akanatha kunditumiza ine ku gehena – mwa kulungama, mwa chilungamo, kunditumiza ine ku gehena – chifukwa cha machimo anga.

Ine sindikuyenera kena kalikonse.

Chikhalidwe changa chonse, kuyambira kuzama kwa chiyambi chake, chili nazo zimenezi – chikuyenera kukhala nazo ndithu.

Ine ndilibe mau akulankhula pakuziyenereza ndi malingaliro a uchimo, kusalankhula kena kalikonse za moyo wodzala ndi tchimo kuyambira pachiyambi kufika pamapeto – inde, moyo wakuchita zinthu mwadala, wowukira, odzala ndi tchimo.

Ena akhoza kuganiza monga angafunire monga mwa kusowa chilungamo cha umuyaya wa chilango cha moyo wa uchimo – kukhumba kwathunthu kugawana pakati pa zaka zochepa za kuchita molakwa ndi zaka zamuyaya za mazunzo mu nyanja ya moto.

Akhoza kuganiza, koma ine ndimakhulupilira, komanso kuvomereza mopanda chikaiko, kuti tchimo limodzi motsutsana ndi Munthu wotere monga Mulungu amene ine ndimamuona pamtanda, ine ndinayenera chilango chosatha mu dzenje lozama la gehena, komanso lamdima.

Inetu sindikulemba ngati munthu amene anaphunzira sukulu ya Baibulo; ndikanakhala kuti ndinatero imeneyi ikanakhala ntchito yosavuta kwa ine kubweretsa malemba ochuluka okonzedweratu kukhala umboni wogwirika wa choonadi cha chilango chosatha.

Komatu ayi; ine ndikulemba ngati munthu amene waphunzitsidwa mwa umulungu choonadi cha mchipululu cha uchimo, ndipo ndilankhula kuti chipululu chimenechi chili, komanso chikhoza kukhala, chosiyidwa kunja kwa kupezeka kwa Mulungu ndi Mwanawankhosa – chilango chamuyaya mu nyanja imene imaotcha ndi moto komanso sufule.

Komatu halleluyah wamuyaya kwa Mulungu wa chisomo chonse! – M’malo mwa kutitumiza ife ku gehena chifukwa cha machimo athu, Iye anatumiza Mwana wake kukhala chiombolo cha machimo athu.

Mu chikonzero chapamwamba chobisika cha chiombolo, ife tikuona Mulungu woyera akuthana ndi funso la machimo athu, ndipo akupereka chigamulo chake pa uchimowo mwa Munthu wake wokondedwa, wamuyaya, Mwana wofana naye, cholinga kuti kusefukira kwa chikondi chake kutsikire pansi pa mitima yathu.

Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu” 1 Yohane 4:10.

Tsopano zimenezi zipereke mtendere ku chikumbumtima, pokhapokha ngati zilandiridwa mwa chikhulupiliro.

Kodi ndi zotheka bwanji kwa munthu kukhulupilira kuti Mulungu wadzikwaniritsa yekha monga mwa machimo ake, ndi kukhala wopanda mtendere?

Ngati Mulungu alankhula kwa ife, “Machimo ako ndi zolakwa zako sindizakumbukiranso,” kodi tifunanso china chiyani monga maziko a mtendere wa chikumbumtima chathu?

Ngati Mulungu wanditsimikizira ine kuti machimo anga onse achotsedwa ngati mtambo wakuda; - kuti aponyedwa kumbuyo kwake – achotsedwa kwamuyaya pamaso pake – kodi sindikuyenera kukhala ndi mtendere?



Ngati Iye wandionetsa munthu amene anasenza machimo anga pamtanda, tsopano anavekedwa ufumu kudzanja lamanja la Chifumu kumwamba, kodi moyo wanga sukuyenera kulowa mu mpumulo wangwiro monga mwa funso la machimo anga? Indedi zikuyenera kutero.

Ndifunseko kuti, kodi Khristu anafika bwanji pamalo pamene Iye tsopano akukhala pa mpando wachifumu wa Mulungu? Kodi anafika monga Mulungu wa zonse, wodalitsika kwamuyaya?

Ayi ndithu; pakuti Iye anali choncho kale.

Kodi anafika monga Mwana wamuyaya wa Atate?

Ayi ndithu; Iyetu anali kale chomwecho – kukhalabe m’chifukato cha Atate – chithunzithunzi cha umuyaya wa Atate ndi chisangalalo chosasimbika.

Kodi chifukwa chinali kuti anali wopanda banga, woyera, munthu wangwiro, amene chilengedwe chake chinali choyera, chosakhudzana ndi tchimo?

Ayi ndithu; pakuti mu chikhalidwe chimenechi, komanso pa maziko amenewa, Iye akanatha mu nyengo iliyonse, pakati pa modyera ng’ombe ndi mtanda, kutenga malo kudzanja lamanja la Mulungu.

Kodi nanga zinakhala bwanji?

Malemekezo amuyaya apite kwa Mulungu wa chisomo chonse! zinali monga Iye amene mwa imfa yake anakwaniritsa ntchito ya ulemelero wa chiombolo – Iye amene anaimilira ndi kugamulidwa ndi mtolo onse wa machimo athu – Iye m’modzi amene anakwaniritsa kulungama konse kwa mpando wachifumu umene Iye tsopano akukhalapo.

Imeneyi ndi mfundo yaikulu ndi yofunikira kuti muwerengi wokhudzika ayigwire.

Singalephere kumasula mtima ndi kubweretsa bata mu chikumbumtima.

Ifetu sizingatheke kumutenga mwa chikhulupiliro Munthu amene anakhomedwa pa mtengo, tsopano anakhazikitsidwa pa mpando wachifumu, ndi kukhalabe wopanda mtendere ndi Mulungu.

Ambuye Yesu Khristu, atatenga pa Iye yekha machimo athu, komanso chiweruzo kulingana ndi machimowo, Iye sakanakhala kumene aliko tsopano ngati limodzi mwa machimowo likanakhala osawomboledwa.Kuonerera wonyamula machimo athu akuvekedwa ufumu ndi ulemelero ndiko kuona machimo athu kuchotsedwa kwamuyaya mwa kupezeka kwa umulungu.

Kodi machimo athu ali kuti?

Machimo onse anachotsedwa kwathunthu.

Kodi timadziwa bwanji zimenezi?

Iye amene anawatenga machimowo pa Iye yekha anadutsa m’mwamba ndi kufika pansonga penipeni pa ulemelero.

Chilungamo chamuyaya chazungulira chikope chake chodalitsika chokhala ndi kolona wa ulemerero, monga Wokwaniritsa wa chiombolo chathu – Wotinyamulira machimo athu;

Khristu wovekedwa ufumu, komanso chikumbumtima chabwino, mwa choonadi chodalitsika cha chisomo, chimene chili chosalekanitsika.

Mfundo yodabwitsa! Tiyeni tikuwe ndi mphamvu zathu zonse zowomboledwa mayamiko a chikondi chake chopulumutsa.

Tiyeni tione momwe choonadi chotonthoza chimenechi chaikidwira m’Malemba Woyera.

Ku Aroma 3:21-26 timawerenga, “Koma tsopano chilungamo cha Mulungu, chaoneka chopanda lamulo, chilamulo ndi aneneri achitira ichi umboni; ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiliro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupira; pakuti palibe kusiyana; pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemelero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu; amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiliro cha m’mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m’kupereka kwake analekelera machimo ochitidwa kale lomwe; kuti aonetse chilungamo chake m’nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupilira Yesu.”

Komanso ku Aroma 4:23-25, akulankhula za chikhulupiliro cha Abrahamu chimene chinawerengedwa kwa iye mwa chilungamo, mtumwi akuonjezera, “Ndipo ichi sichinalembedwa chifukwa cha iye yekha yekha kuti chidawerengedwa kwa iye; koma chifukwa cha ifenso kwa ife amene chidawerengedwa kwa ife amene tikhulupira iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu, amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama

Pamenepa tili naye Mulungu kuonetsedwa ku mizimu yathu monga Iye amene anaukitsidwa kwa akufa Iye wotisenzera machimo athu.

Kodi anachitiranji zimenezi?

Chifukwa Iye amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu wamkweza Iye mwangwiro ku ulemelero kulemekeza zolakwa zimenezi ndi kuzitaya kwamuyaya.

Mulungu sanangotumiza Mwana wake wokondedwa padziko lapansi, koma anamupweteka Iye chifukwa cha zochimwa zathu, ndi kumuukitsa Iye kwa akufa, cholinga kuti tikadziwe ndi kukhulupilira kuti zochimwa zathu zonse zinachotsedwa munjira yakuti tikalemekeze Iye mopanda malire ndi kwamuyaya.



Kumvera kwamuyaya ndi kwathunthu kudzina lake!

Komatu tili ndi umboni woonjezera pa choonadi chachikulu chimenechi.

Ku Aheberi 1:1-3 timawerenga mau otakasa ngati awa:

Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana [Wake] amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am’mwamba omwe; ameneyo pokhala ndi chinyezimiro cha ulemelero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m’mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu m’Mwamba.”

Ambuye wathu Khristu, dzina lake lilemekezeke, sakanatenga malo ake pa mpando wachifumu wa Mulungu, kufikira atadzipereka yekha pa mtanda, kuyeretsa machimo athu.

Komabe Khristu woukitsidwa kudzanja lamanja ndiwo umboni wa ulemelero ndi wosakaikitsa kuti machimo athu onse achotsedwa, pakuti Iye sakanakhala kumene Iye ali lero ngati tchimo lina mwa machimowo likanatsalira.

Mulungu anaukitsa kwa akufa Munthu yemweyo amene Iye mwini anaikapo mtolo onse wa machimo athu.

Machimo onse anathetsedwa – mwa umulungu, kuthetsedwa kwamuyaya.

Nzosatheka kuti tchimo ngakhale limodzi likapezeke mwa m’bale wofooka mwa Yesu, monga silingakhalire mwa Yesu mwini.

Chimenechi ndi chinthu chodabwitsa kuchilankhula, koma ndi choonadi cholimba cha Mulungu, chokhazikitsidwa m’malo osiyanasiyana mu Malemba Woyera; ndipo moyo umene ungakhulupilire ukapeze mtendere umene dziko lapansi sungapereke kapena kuchotsa.

GAWO 2.

Kufikira pamenepa, tadzadzidwa ndi maonedwe otere a ntchito ya Khristu imene imayankha funso lokhudza kukhululukidwa kwa machimo; ndipo ife tikukhulupilira kuti muwerengi wamvetsetsa ndi kukhazikika pa mfundo yaikulu imeneyi.

Umenewu ndi ufulu wa chisangalalo chake, ngati iye adzamtenga Mulungu mwa Mau ake.

Amene Khristu anawavutikira.

Machimo, wolungama chifukwa cha wosalungama, kuti akatibweretse ife kwa Mulungu.”

Ngati Khristu anazunzika chifukwa cha machimo athu, kodi sitikuyenera kudziwa kudalitsika kozama kwakukhala omasulidwa kwamuyaya kuchoka ku chipsinjo cha machimo?

Kodi zikhoza kukhala molingana ndi lingaliro komanso mtima wa Mulungu kuti iye amene Khristu anamuzunzikira akhalebe mu goli lokhazikika, kumangidwa ndi unyolo wa machimo ake, ndi kulirabe sabata ndi sabata, mwezi ndi mwezi, komanso chaka ndi chaka, kuti mtolo wa machimo ake kukhala osakhululukidwa?

Ngati malankhulidwe otere ndi owona komanso oyenera kwa Akhristu, nanga Khristu anachita chiyani kwa ife?

Kodi zikhoza kukhala zoona kuti Khristu anachotsa machimo athu, komabe ife nkukhala omangidwa ndi maunyolo ake?

Kodi ndi zoona kuti Iye anatenga mtolo wolemera wa machimo athu, ndipo ife tidakapsinjikabe pansi pa kulemera kosakhulukidwa kwa machimowo?

Anthu ena adzasangalatsidwa kutikopa ife kuti nkosatheka kudziwa kuti machimo athu anakhululukidwa; cholinga kuti ife tikhalebe osadziwa mpaka kumapeto a moyo wathu za kufunika kwa funso lapamwamba limeneli.

Ngati zimenezi zili choncho, kodi uthenga wa mtengo wapatali wa chisomo cha Mulungu – uthenga wa chipulumutso udzakhala wotani?

Pachifukwa cha chiphunzitso choipa ngati chimenechi, kodi mau a Paulo mtumwi wodalitsika anatanthauza chiyani ku kachisi ya Antiokeya?

Potero padziwike ndi inu amuna abale, kuti mwa iye [Yesu Khristu, wakufa ndi kuukitsidwa] chilalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo; ndipo mwa iye yense wokhulupira ayesedwa [osati adzayesedwa] wolungama kumchotsera zonse zimene simungathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.” Machitidwe 13:38, 39.

Ngati timatsamira pa lamulo la Mose, pa kusunga kwathu malamulo, pakuchita ntchito zathu, pakumva monga ife tifunira, pakulemekeza Khristu ndi kumukonda Mulungu monga ife tifunira, chifukwa chikhala kuti ife tikhalebe wokaika komanso mu mdima wosadziwa kanthu, kuti tisakhale ndi kuthekera kokhala pa maziko a chitsimikizo.

Tikadakhala kuti tili ndi changu monga chikope cha diso chichitira mu nkhani imeneyi, pamenepo zoonadi tikanakula kwambiri kumbali yathu pakuganizira za chitsimikizo.

Koma mbali inayi, pamene timva liwu la Mulungu wa moyo amene sanganame, kulengeza m’makutu mwathu uthenga wabwino kuti kudzera mwa Mwana wake wokondedwa amene anafera pamtanda, anaikidwa m’manda, naukitsidwa kwa akufa, ndipo akukhala mu ulemelero – kuti kudzera mwa Iye popanda zimene zili zathu – kudzera mwa Iye wodzipereka yekha kamodzi kwamuyaya, kudzadza ndi kukhululukidwa kwa machimo kwamuyaya kwalalikidwa, monga choonadi cha makono, kuti tsopano moyo ulionse usangalale umene ukhulupilira mu nkhani ya mtengo wapatali ya Mulungu, kodi zingatheke bwanji aliyense kupitilira kukaika ndi kusatsimikizika?

Kodi ntchito ya Khristu inatsirizika?

Iye akutero inatsirizika.

Kodi anachita chiyani?

Iye anachotsa machimo athu.



Kodi machimo anachotsedwa, kapena adakali pa ife – chenicheni ndi chiti?

Muwerengi, nenani chenicheni ndi chiti?

Kodi machimo anu ali kuti?

Kodi anachotsedwa ngati mtambo wakuda?

kapena anakhazikikabe ngati katundu wolemera wa chikumbumtima, mu mphamvu ya kutsutsa chikumbumtima chanu?

Ngati sanachotsedwe ndi imfa yowombola ya Khristu, amenewo sadzachotsedwanso.

Ngati Iye sanawatenge pa mtanda, inuyo mudzawatengabe kufikira ku mazunzo a malawi a moto ku gehena kwamuyaya.

Inde; khalani otsimikizika pa zimenezi, palibenso njira ina yoyankhira funso ili lolemetsa komanso la kanyengo kochepa.

Ngati Khristu sanathetse vuto limeneli pa mtanda, inutu mukuyenera kulithetsa noka ku gehena.

Zikuyenera kukhala choncho, ngati mau a Mulungu akuyenera kukhala owona.

Koma ulemelero upite kwa Mulungu, umboni wake ukutitsimikizira ife kuti Khristu anavutika kamodzi chifukwa cha machimo, wolungama kwa osalungama, kuti Iye akatifikitse ife kwa Mulungu; osati kungotipititsa ife kumwamba pamene tidzafa, koma kutibweretsa ife kwa Mulungu tsopano kodi amatibweretsa bwanji kwa Mulungu?

Womangidwa ndi maunyolo a machimo athu?

wokhala ndi mtolo wosachoka wa chikumbumtima m’moyo mwathu?

Ayi ndithu, kunena zoonadi; Iye amatibweretsa kwa Mulungu wopanda banga kapena mlandu ulionse.

Iye amatibweretsa kwa Mulungu mu kutilandira kwake konse.

Kodi muli kutsutsidwa kwina kulikonse mwa Iye?

Ayi ndithu; munalibe, dzina lake lidalitsike, pamene Iye anaimilira m’malo mwathu, tchimo linachokeratu kwamuyaya – kutayidwa m’madzi akuya a chikhululukiro cha umulungu.

Iye anagamulidwa ndi machimo athu, pa mtanda.

Mulungu anaika pa Iye zolakwa zathu zonse, ndipo anathana ndi Iye chifukwa cha machimowo.

Funso lonse la machimo athu, molingana ndi maonedwe a Mulungu, linachotsedwa kwathunthu, chifukwa linathetsedwa pakati pa Mulungu ndi Khristu, kudzera mu mthunzi owopsa wa pamtanda.

Inde zonse zinachitika, kamodzi ndi kwamuyaya.

Kodi timadziwa bwanji zimenezi?

Mwa ulamuliro wa Mulungu yekhayo woona.

Mau ake amatitsimikizira kuti ife tili ndi chiombolo kudzera m’mwazi wa Khristu, kukhululukidwa kwa machimo, molingana ndi kulemera kwa chisomo chake.

Iye akutiuza ife, mwa kukoma kwa mau, mwa chifundo cholemera ndi chakuya, kuti machimo athu ndi zolakwa zathu Iye sazakumbukiranso.

Kodi zimenezi sizokwanira?

Kodi tikuyenera kupitilira kulira kuti ife tatopa ndi kumangidwa ndi maunyolo a machimo athu?

Kodi tikuyenera kudetselera ntchito yangwiro ya Khristu?

Kodi tiononge kukongola kwa chisomo cha umulungu ndi kupereka bodza ku umboni wa Mzimu Woyera mu malemba a choonadi?

Tiganize mozama! Sizikuyenera kukhala choncho.

Tiyeni m’malo mwake tikwezeke ndi chiyamiko mdalitso woperekedwa kwaulere kwa ife mwa chikondi cha umulungu, kudzera m’mwazi wopambana wa Khristu.

Chimwemwe cha mtima wa Mulungu ndicho kukhululukira machimo athu, inde, Mulungu amasangalala pa kukhululukira machimo ndi zoipa.

Zimenezi zimamulimbikitsa komanso kumulemekeza Iye kuthira mafuta ake onunkhira a mtengo wapatali mu mtima wosweka ndi wodzipereka mwa chikondi ndi chifundo chake chokhululukira.

Iye sanakaniza Mwana wake, koma anamupereka, ndipo anamuvulaza pa mtengo wotembereredwa, cholinga kuti akakwanitse, mwa chilungamo chake changwiro, kulola mtsinje wa chisomo kuyenda kuchokera mu mtima wake waukulu, wachikondi, kupita kwa osauka, otsutsika, odziononga okha, ochimwa, ozunzidwa ndi chikumbumtima.

Komabe ngati muwerengi akumva kuti afufuzebe momwe angapezere chitsimikizo chimene kukhululukidwa kwa machimo kodalitsikaku – chipatso cha chiombolo cha Khristu zimayendera, ndi kugwilira ntchito mwa iye, akuyenera kumvera mau amene akuchokera pa milomo ya Mpulumutsi woukitsidwa, pamene Iye amakhazikitsa uthenga woyambilira wa chisomo chake.

Ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; ndi kuti kulalikidwe mdzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse kuyambira ku Yerusalemu.” Luka 24:46, 47.

Pamenepa tili ndi utumiki waukulu komanso waulemelero – m’maziko ake, mu ulamuliro wake, maozungulira mwake. Khristu anazunzika.

Amenewa ndi maziko operekedweratu a kukhululukidwa kwa machimo.

Popanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo.

Komatu mwa kukhetsa mwazi, ndipo mwa mwazi wokhawu, pali kukhululukidwa kwa machimo – kukhululukidwa kwathunthu monga mwazi wa mtengo wapatali wa Khristu ukukwanira kuchita zimenezi.

Koma kodi ulamuliro uli kuti?

Kwalembedwa.”

Ulamuliro wodalitsika, wosatsutsika! Ndipo palibe chingagwedeze ulamulirowu.

Inetu ndikudziwa, mwa ulamuliro olimba wa Mau a Mulungu, kuti machimo anga onse akhululukidwa, onse anachotsedwa, onse anachoka kwamuyaya, onse anachotsedwa kumbuyo kwa Mulungu, cholinga kuti mwa kuthekera kwina kulikonse asakatsutsane ndi ine.

Pomaliza, monga mwa zotizungulira.

Ndiwo “maiko onse.”

Pamenepa akuphatikizirapo ineyo, popanda kufunsa kulikonse.

Pamenepa palibe kusiyapo, palibe zoyenera kuchita munthu, kapena maphunziro.

Uthenga wodalitsika unayenera kunyamulidwa pa mapiko a chikondi ku mitundu yonse – kudziko lonse – ku cholengedwa chilichonse pansi pa thambo.

Kodi ine ndikhoza kudzichotsa bwanji pa utumiki umenewu wadziko lonse lapansi?

Kodi ndikuyenera kudzifunsa mwa kanthawi, kuti kuwala kwa dzuwa la Mulungu kunapangidwira ineyo?

Ayi ndithu sizikuyenera kutero.

Nanga ndifunsiranji mfundo ya mtengo wapatali ya kukhululukidwa kwa machimo anga?

Sindikuyenera kutero ngakhale pang’ono.

Chikhululukiro ndi changa monga kuti ine ndinali wochimwa yekhayo pansi pa kuphimba kwa kumwamba kwa Mulungu.

Uthunthu wake wa kaonedwe umatsekereza mafunso onse monga zopangidwira ine.

Zoonadi ngati chilimbikitso china chinafunika, chikupezeka mu mfundo yakuti akazembe odalitsika anayenera “kuyambira ku Yerusalemu” – chisonyezo cha kutsutsika kwakukulu pa nkhope ya dziko lapansi.

Iwo anayenera kupereka chikhululukiro choyambilira kwa iwo amene anapha Mwana wa Mulungu.

Zimenezi anachita mtumwi Petro mu mau aja a chisomo chabwino ndi chopambana, “Kuyambira ndi inu, Mulungu ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwenzani yense ku zoipa zake” Machitidwe 3:26.

Nzosatheka kupeza chinthu china chopeza bwino kapena chodzadza, kapenanso chokongola kuposa chimenechi.

Chisomo chimene chinafikira iwo amene anapha Mwana wa Mulungu, chingathe kufikira wina aliyense.



Mwazi umene unayeretsa kutsutsika kwa mlandu wotere ungathenso kuyeretsa wochimwa wopanda phindu kunja kwa malire a gehena.

Muwerengi wachidwi, kodi mukukaikabe za chikhululukiro cha machimo anu?

Khristu anazunzikira machimo

Mulungu amalalikira za kukhululukidwa kwa machimo.

Iye akulonjeza mau ake pa mfundoyi.“Kwa iye anapatsa aneneri onse umboni, kuti kudzera mu dzina lake yense wakukhulupilira mwa iye alandire chikhululukiro cha machimo.”

Kodi china ndi chiyani chimene mukadakhala nacho?

Kodi mukhaliranji wokaika ndi wonyalanyaza?

Kodi mukudikira chiyani?

Inutu muli nayo ntchito yotsirizika ya Khristu komanso mau okhulupirika a Mulungu.

Zoonadi zimenezi zikwaniritse mitima yanu komanso kumasula malingaliro anu.

Tikulimbikitsani inu kuti muvomereze kukhululukidwa kwathunthu ndi kwamuyaya kwa machimo anu onse.

Landirani mu mtima mwanu uthenga wokoma wa chikondi cha umulungu ndi chifundo, ndipo yendani munjira yanu mosangalala.

Imvani mau a Mpulumutsi woukitsidwa, kulankhula kuchokera pa mpando wa chifumu kumwamba, kukutsimikizirani kuti machimo anu onse akhululukidwa.

Lolani mau enieni ochokera mkamwa mwa Mulungu mwini, kugwa mu mphamvu yakumasula pa mzimu wanu wosautsika, “Machimo anu ndi zolakwa zanu sindizakumbukiranso.”

Ngati Mulungu akulankhula kwa ine; ngati Iye akunditsikimizira choncho kuti sadzakumbukiranso machimo anga, kodi sindikuyenera kukwanitsidwa kwathunthu ndi kwamuyaya?

Nanga ndikhaliranji wokaika ndi wolingalira pomwe Mulungu walankhula?

Kodi chimene chingapereke chitsimikizo ndi chiyani komatu mau a Mulungu amene ndi amoyo komanso okhala kwamuyaya?

Amenewa ndiwo maziko a chitsimikizo; ndipo palibe mphamvu ya padziko kapena ku gehena, umunthu kapena matsenga zingathe kuwagwedeza.

Ntchito yotsirizika ya Khristu komanso mau okhulupirika a Mulungu ndiwo maziko komanso ulamuliro wa kukhululukidwa kwathunthu kwa machimo.

Komatu, alemekezeke kwamuyaya Mulungu wa chisomo chonse, sikukhululukidwa kwa machimo kokha kumene kukulengezedwa kwa ife kudzera mu imfa yowombola ya Khristu.

Chimenechi mwa icho chokha chingathe kukhala chopempha ndi mdalitso waukulu kwambiri; ndipo monga umo taonera, timasangalala nawo molingana ndi kukula kwa mtima wa Mulungu, komanso molingana ndi phindu komanso mphamvu ya imfa ya Khristu, monga Mulungu amawerengera.

Komatu pambali pa kukhululukidwa kwa machimo kwathunthu ndi kwa ngwiro, tilinso ndi

MAMASULIDWE ATHUNTHU KUCHOKA KU MPHAMVU YA UCHIMO YOPEZEKA TSOPANO.

Imeneyi ndi mfundo yaikulu kwa munthu aliyense wokondadi chiyero.

Molingana ndi chisomo cha ulemelero, ntchito yomweyo imene yatetezera kumasulidwa kwathunthu kwa machimo yaphwanyanso kwamuyaya mphamvu ya tchimo.

Sikungoti machimo a m’moyo achotsedwa, koma tchimo la chikhalidwe ladzudzulidwa.

Wokhulupilira ali nawo mwayi wakudziyesa yekha ngati wakufa ku uchimo.

Iye angathe kuimba ndi mtima wokondwera,

Kwa ine, Ambuye Yesu, wandifera, Ndipo ine ndafa mwa Iye; Inu mwauka, maunyolo anga amasulidwa, Ndipo Inu mukukhalira mwa ine. Nkhope ya Atate yowala mwa chisomo ikuwala tsopano pa ine.”

Kumeneku ndiye kupuma koyenera kwa Mkhristu.

Ine ndinapachikidwa ndi Khristu, sindinenso amene ndikukhala; koma Khristu wakukhala mwa ine.”

Chimenechi ndiye Chikhristu.

Ine” wakale anapachikidwa, ndipo Khristu ali wamoyo mwa ine.

Mkhristu ndiye wolengedwa watsopano.

Zakale zapita.

Imfa ya Khristu inatseka kwamuyaya mbiri ya “ine” wakale; ndipo ngakhale tchimo likhala mwa wokhulupilira, mphamvu yake inaonongedwa ndi kuchotsedwa kwamuyaya.

Osangoti kutsutsika kwake kokha kunachotsedwa, komanso kukhazikika kwake koipa kunachotsedwa kwathunthu.

Chimenechi ndi chiphunzitso cha ulemelero cha Aroma 6-8.

Wophunzira wanzeru wa kalata ya pamwamba imeneyi akuwona za chimenechi, kuchokera ku Aroma 3:21 kufika ku Aroma 5:11, ife tili ndi ntchito ya Khristu yochitika pa funso la machimo.

Komanso pa mutu 5:12 kufika kumapeto a mutu 8.

Tili nawonso mawonedwe ena a ntchito imeneyi, kunena kuti, machitidwe ake pa funso la tchimo – “munthu wathu wakale” – “thupi la tchimo” – “tchimo mu thupi.”

Mulibe m’malemba nkhani yokhudza kukhululukidwa kwa machimo.

Mulungu analitsutsa tchimo, osati kulikhululukira – imeneyi ndi mfundo yofunikira kwambiri.

Mulungu anakhazikitsa udani wake waukulu pa tchimo, mu mtanda wa Khristu.

Iye anaonetsa ndi kuchita chigamulo pa tchimolo; ndipo tsopano wokhulupilira angathe kudziona yekha ngati wolumikizidwa ndi Iye amene anafa pa mtanda, ndipo waukitsidwa kwa akufa.

Iye anadutsa mu nyengo ya kukhazikika kwa uchimo nalowa mu nyengo yatsopano ndi yodalitsika imene chisomo chimalamulira kudzera mu kulangama.

Koma ayamikidwe Mulungu,” akutero mtumwi, “kuti ngakhale mudakhala [kalelo, koma tsopano simuli choncho] akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho. (Malire.) Ndipo pamene munamasulidwa ku uchimo [osati kungokhululukidwa machimo], munakhala akapolo a chilungamo. Ndilankhula manenedwe a anthu chifukwa cha kufooka kwathupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusayeruzika kuti zichite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso. Pakuti pamene inu munali akapolo a uchimo, munali osatumikira chilungamo. Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m’zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa. Koma tsopano, pamene munamasulidwa ku uchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.” Aroma 6:17-22.

Pamenepa pali chinsinsi chapamwamba cha kukhala m’chiyero.

Ifetu tinafa mu uchimo; ndipo tili ndi moyo kwa Mulungu.

Ulamuliro wa uchimo unatha.

Kodi uchimo umachita chiyani kwa munthu wakufa? Palibe.

Pamenepo wokhulupilira anafa pamodzi ndi Khristu; anaikidwa pamodzi ndi Khristu; anaukitsidwa ndi Khristu, kuti akayende moyo watsopano.

Iye amakhala pansi pa ulamuliro wa mtengowapatali wa chisomo, ndipo iye ali nacho chipatso chake cha chiyero.

Munthu amene amapeza ponamizira kuchokera ku chisomo chochuluka cha umulungu nkumakhalabe mu uchimo, amakana maziko a Chikhristu.

Kodi zitheka bwanji ife amene tinafa ku uchimo, nkumakhalabe mu uchimowo?” Zosatheka.

Zimenezi zikhoza kukhala kukana maziko a Chikhristu.

Kuganiza kuti Mkhristu ndi munthu amene akuyenera tsiku ndi tsiku, sabata ndi sabata, mwezi ndi mwezi, komanso chaka ndi chaka, kumachimwabe ndi kumalapa, ndiko kunyozetsa Chikhristu komanso kupangitsa Chikhristu chonse kukhala chabodza.

Kunena kuti Mkhristu akuyenera kumachimwabe chifukwa ali mthupi ndiko kukana imfa ya Khristu kumbali ina yaikulu, komanso kupangitsa chiphunzitso cha mtumwi ku Aroma 6-8 kukhala chabodza.

Tiyamika Mulungu, palibe choyenera mwanjira ina iliyonse kuti wokhulupilira akuyenera kumachimwa.

Ana anga, ndakulemberani zinthu izi kuti musachimwe.”

Tisadzilungamitse tokha mu lingaliro lina lililonse la uchimo.

Cholowa chathu chokoma ndicho kuyenda mkuwala, monga Mulungu ali mkuwala; ndipo zoona zake, pamene ife tiyenda mkuwala, sitimachimwa ayi.

Zoopsa! Ife timachoka mkuwala ndi kukachimwa; koma lingaliro loona, la umulungu la Mkhristu ndilo, kuyenda mkuwala, ndi kusachimwa.

Lingaliro la uchimo ndi lachilendo kwa Mkhristu weniweni.

Ifetu tili ndi uchimo, ndipo tidzakhala nalobe pokhapokha pamene tili mthupi: koma tikayenda mu Mzimu, tchimo lokhala mu chikhalidwe chathu silidzaonekera m’moyo mwathu.

Kulankhula kuti sitikuyenera kuchimwa, ndiko kulankhula za cholowa cha mkhristu; kulankhula kuti sitingachimwe ndicho chinyengo komanso bodza lalikulu.

GAWO 3.

Kuchokera mu zimene tadutsa kale, tikuphunzira kuti zotsatira zazikulu za ntchito ya Khristu kalelo ndiko kutipatsa ife kuima kwabwino pamaso pa Mulungu.

Iye anawayenereza kwamuyaya kuti iwo ndi wolungamitsidwa”

Iye wationetsera ife mu Kupezeka kwa Umulungu, mwa kuvomereza kwake kwangwiro, mu ubwino onse ndi chikhalidwe cha dzina lake, Umunthu wake, komanso ntchito yake; kuti monga mtumwi Yohane akulankhula, “Chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m’dziko lapansi” 1 Yohane 4:17.

M’menemu ndi momwe anakonzera maimidwe a mwanawankhosa wofooka mwa mwazi wakugula gulu la nkhosa la Khristu.

Kapena zikhoza kukhala munjira ina.

Zikuyenera kukhala zimenezi kapena kuonongeka kwa uzimu kwamuyaya.

Palibe kutalika kwa tsitsi pakati pa choonadi chimenechi changwiro pamaso pa Mulungu komanso choyenera kuchita pa kutsutsika ndi chionongeko.

Ifetu tili m’machimo athu, kapena mwa Khristu woukitsidwa.

Palibe kukhala pakatikati.

Ifetu takutidwa ndi kutsutsika, kapena takutidwa kwathunthu mwa Khristu.

Koma wokhulupilira analengezedwa, mwa mau a ulamuliro a Mzimu Woyera mu malemba, kukhala “wathunthu mwa Khristu” – “Wangwiro potengera chikumbumtima chake” – “woyenerezedwa mu umuyaya” – “Kukonza kulumikizidwa kulikonse” – “kulandiridwa mwa wokondedwa” – “Kupangidwa [kapena kukhala] chilungamo cha Mulungu mwa Khristu.”

Ndipo zonsezi kudzera mu nsembe ya pamtanda.

Imfa yowombola ya mtengo wapatali ya Khristuyi imakonza maziko olimba ndi osatsutsika a maziko a Chikhristu.

Munthu ameneyu, atapereka nsembe imodzi ya machimo, kwamuyaya anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu.”

Khristu wokhala kudzanja lamanja ndiye chitsimikizo cha ulemelero komanso tanthauzo langwiro la malo a wokhulupilira pamaso pa Mulungu.

Ambuye wathu Yesu Khristu, atalemekeza Mulungu pa machimo athu, ndipo anatenga chiweruzo cha Mulungu pa ife monga ochimwa, watikhazikitsa monga mwa chiyanjano cha moyo ndi Iye mwini, kumalo osati mwa chikhululukiro, kuvomerezedwa, ndi mtendere, komatu omasulidwa kwathunthu kuchoka mu goli la uchimo – malo a chipambano chotsimikizika pa zonse zimene zikhoza kukhala zotsutsana nafe, kaya ndi tchimo lokhala mkati mwathu, mantha a Satana, lamulo, kapena dziko ili loipa.

Tibwerezanso, kumeneku ndiko kukhululukidwa kwathunthu kwa wokhulupilira, ngati tingaphunzitsidwe monga mwa Malembo Woyera.

Ndipo tikupempha muwerengi wa Chikhristu kuti asasangalatsidwe ndi zina zochepera pamenepa.

Iye asavomerezenso chiphunzitso chonyenga chimene chikupezeka pakati pa Akhristu ena, komanso ndi madongosolo ake a chipembedzo, zimene zimangotengera moyo kubwereranso ku mdima, kutalikira, ndi msinga za Chiyuda – chikonzero chimene Mulungu anachipenzera vuto, chimene anachithetsa kwamuyaya, chifukwa sichinakwaniritse chikhumbokhumbo cha malingaliro ake oyera, kapena kukwaniritsa mtima wake wokonda, pakupereka kwa wopembedza mtendere wangwiro, ufulu wangwiro, kukhala naye chifupi kwangwiro, ndipo zimenezi kuchitika kwamuyaya.

Ife tikupempha anthu onse a Mulungu, kumbali zonse zimene amavomereza mpingo, awonenso mbali imene iwo ali, komanso aone kuti amamvetsetsa bwanji ndi kusangalala mu Chikhristu chimene iwo ali, monga mwa kulembedwa kwa malemba amene ayikidwa, komanso amene akhoza kuchulukitsidwa mazanamazana.

Asiyeni asiyanitse mwachidwi ndi mokhulupirika ziphunzitso za chipembedzo ndi Mau a Mulungu, ndipo onani kuti akugwirizana pati.

Munjira imeneyi iwo akapeza momwe Chikhristu chalero chimachitira mosemphana ndi chiphunzitso cha moyo cha m’Chipangano Chatsopano; ndipo zotsatira zake, miyoyo ikulandidwa cholowa chimene ili nacho ngati Akhristu, ndipo akusungidwa mu chikhalidwe chimene chili ndi zochitika za chilamulo cha Mose.

Zonsezi ndi zokhumudwitsa kwambiri.

Zimamvetsa chisoni Mzimu Woyera, zimadzetsa mabala mu mtima wa Khristu, zimanyozetsa chisomo cha Mulungu ndipo zimasemphana ndi ndime zomveka bwino za m’Malemba Woyera.

Ife tili ndi chitsimikizo kuti mizimu ya anthu ochuluka zedi nthawi ino ikupangitsa mtima kutulutsa magazi; ndipo zimenezi zimaoneka kwambiri mu chiphunzitso cha zipembedzo, zikhulupiliro zawo ndi ndondomeko zawo.

Kodi muzipeza kuti, pakati pa maudindo wamba a mu Chikhristu, munthu kukhala mu chisangalalo cha chikumbumtima choyera mwangwiro, cha mtendere ndi Mulungu, chosamalidwa ndi Mzimu?

Kodi sizoona kuti anthu akuphunzitsidwa poyera komanso mwadongosolo kuti ndi chapatali kwa wina aliyense kunena kuti machimo ake onse anakhululukidwa – kuti ali ndi moyo wosatha – kuti iye analungamitsidwa ku zinthu zonse – kuti iye anavomerezedwa mwa chikondi – kuti anatsindikizidwa ndi Mzimu Woyera – kuti iye sangatayike, chifukwa anayanjanitsidwa ndi Khristu kudzera mwa Mzimu wakukhala mwa iye?

Kodi zimenezi sizolowa za Chikhristu kukanidwa ndi kunyalapsidwa mu Chikhristu?Kodi anthu sanaphunzitsidwe kuti ndi zoopsa munthu kukhala ndi chiyembekezo chachikulu – kuti ndi kwabwino munthu kukhala wokayikira ndi wamantha – ndipo chiyembekezo chimene tikuyenera kukhala nacho ndi chakuti tidzalowa kumwamba pamene ife tidzafa?

Kodi miyoyo ikuphunzitsidwa kuti za choonadi cha ulemelero kulumikizana ndi kulengedwa kwatsopano?

Kodi iwo azikika ndi kuimikika pati mu chidziwitso cha kuima kwawo mu kuuka ndi kukwezedwa kwa Mutu kumwamba?

Kodi iwo akutsogozedwa kuti pa zokoma za zinthu zimene Mulungu anapereka kwa ulere kwa anthu ake okondedwa?

Kalanga ine! Kalanga ine! Tikulira kuganizira za yankho lokhalo lowona limene likhoza kuperekedwa ku kufufuza kotereku.

Gulu la nkhosa la Khristu lamwazika m’mapiri a mdima ndi m’mabwinja.

Miyoyo ya anthu a Mulungu yasiyidwa patali pamene pali chikhalidwe cha Chiyuda.

Iwo samadziwa za tanthauzo la chinsalu chong’ambika pakati, za kuwandikana ndi Mulungu, za kulandiridwa mwa Wokondedwa.

Gome la Ambuye lomweli lakutidwa ndi chikhalidwe cha kumidima cha matsenga, ndipo lazungulidwa ndi zikhomo za malamulo a kumidima ndi opondereza.

Chiwombolo chokwanira, kuchotsedwa kwathunthu kwa machimo, kulungamitsidwa kwangwiro pamaso pa Mulungu, kuvomerezedwa mwa Khristu woukitsidwa, Mzimu wodalira, chiyembekezo chowala ndi chodalitsika cha kubwera kwa Mkwati – choonadi chachikulu ndi cha ulemelero chonsechi – zolowa zoperekedwa za Mpingo wa Mulungu – zinasiyidwa pambali ndi ziphunzitso za zipembedzo za chikhristu ndi njira zawo za uzimu.

Ena mwina akhoza kuganiza kuti ife tapereka chithunzithunzi choipa.

Ifetu tikhoza kunena – ndipo tikunena ndi mtima onse – ngakhale kwa Mulungu zikanakhala chomwechi! Ife mantha athu ndi akuti chithunzithunzichi ndi choona chake chenicheni.

Ifetu tili okhutitsidwa kwambiri ndi mfundo yakuti, nyengo imene mpingo osangoti mpingo chabe, koma mazana mazana a nkhosa zenizeni za Khristu ndi yotere, ndipo titazindikira za chimenechi monga momwe Mulungu amaonera, zikuyenera kuswa mitima yathu.

Komabe, tikuyenera kukhazikika pa mutu wathu, ndipo pakuchita chomwechi tikukonza njira yabwino imene ikhoza kuganiziridwa pa nyengo yomvetsa chisoni ya anthu a Mulungu ochuluka.

Ifetu takhazikika pa ntchito ya mtengo wapatali imene Ambuye wathu Yesu Khristu anatikwaniritsira ife, pakuchotsa machimo athu onse, komanso pa kutsutsa tchimo, kutikhazikitsira ife njira ya kachotsedwe ka machimo, komanso kumasulidwa kwathunthu ku machimowo, monga mphamvu yolamulira.



Mkhristu simunthu amene wangokhululukidwa koma kumasulidwanso.

Khristu anamufera iye, ndipo iye anafa mwa Khristu.

Motero iye ndi womasulidwa, monga woukitsidwa kwa akufa, ndi kukhala wamoyo kwa Mulungu, kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.

Iye ndi wolengedwa kwatsopano.

Iye wadutsa mu imfa kupita ku moyo.

Imfa ndi chiweruzo zili kumbuyo kwake, ndiponso ulemelero uli pamaso pake.

Iye amatenga udindo wopanda banga ndi machitidwe wopanda chizimezime.

Tsopano, ngati zonse izi ndi zoonadi zake za mwana wa Mulungu aliyense – ndipo malemba amanena kuti – tikufuna china chiyani?

Palibe chimene tingafune pokhudza udindo, pokhudza pamene tili; pokhudza chiyembekezo.

Pokhudza zonse zimenezi, tili ndi chilungamitso changwiro cha umulungu.

Komatu nyengo yathu siyangwiro, mayendedwe athu siangwiro.

Ifetu tidakali mthupi, wozungulidwa ndi zoyipa zosiyanasiyana, kuonetsedwa ndi mayesero osiyanasiyana, ofuna kutigwetsa, kutichotsa pamaso pa Mulungu.

Ifetu patokha sitingathe kuganiza maganizo olondola, kapena kudzikhazika tokha mwa kamphindi pamalo wodalitsika amene chisomo chinatiyikapo.

Zoonadi zimenezi, ifetu tili ndi moyo wosatha, ndipo ife talumikizidwa ndi Mutu wamoyo kumwamba, mwa Mzimu Woyera kutumizidwa padziko lapansi, cholinga kuti tikakhale wotetezeka kwamuyaya.

Palibe chimene chidzagwira moyo wathu, pokhapokhapo ngati “wabisika ndi Khristu mwa Mulungu.”

Komatu pamene palibe chimene chingakhudze moyo wathu, kapena kusokoneza kuima kwathu, pakuona kuti nyengo yathu ndi yodetsedwa, komanso mayendedwe athu odetsedwa, chiyanjano chathu chikuyenera kukhala chosokonezeka, ndipo pamenepa timafunikira

NTCHITO YATSOPANO YA KHRISTU KWA IFE.

Yesu akukhala kudzanja lamanja la Mulungu chifukwa cha ife.

Kulowelera kwake m’malo mwathu sikunayimepo ndi tsiku limodzi lomwe.

Iye anadutsa m’mwamba, mwa chikhalidwe cha kukwaniritsa chiombolo, ndipo kumeneko akutenga udindo wotiyimira ife pamaso pa Mulungu.

Iye ali kumeneko monga wotitengerabe chilungamo chathu, kutikhazikabe ife mu ungwiro wa umulungu ndi chiyanjano chimene imfa yake ya chiombolo inatitengera ife.

Chomwecho ife timawerenga, ku Aroma 5:10, “Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.”

Komanso, ku Ahebri 4:14-16, timawerenga, “Popeza tsopano tili naye Mkuluwansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu. Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi ya kusowa.”

Komanso ku Ahebri 7:24,25 “Koma iye chifukwa kuti akhala iye nthawi yosatha ali nawo unsembe wosasinthika, kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.”

Ndipo ku Ahebri 9:24 “Pakuti Khristu sanalowa m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m’Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.”

Kenako mu kalata woyamba w`a Yohane 2:1,2, tili ndi mutu wofanana umene waperekedwa pansi pa maonedwe osiyaniranako. “Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama; ndipo iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.”

Kodi zonsezi zikhoza kukhala bwanji za mtengo wapatali kwa Mkhristu wa mtima weniweni amene ali ndi chikumbumtima chakuya komanso chikumbumtima chowawa – cha kufooka kwake, kusowa kwake, zolakwa zake ndi kulephera kwake?

Momwe ife tikhoza kufufuzira mwa lamulo, kodi ndi zotheka kwa wina aliyense, maso ake atalunjika pa malemba amenewa monga analembedwera, kusanena kanthu za chikumbumtima cha iye mwini, zokhudza makhalidwe ndi mayendedwe ake osalungama, kukhala ndi funso la chokhumba cha Mkhristu pa utumiki wopitilira wa Khristu m’malo mwake.

Kodi sizosangalatsa kuti muwerengi aliyense wa Kalata ya Ahebri, owonelera aliyense wa nyengo ndi mayendedwe a wokhulupilira wochita bwino zedi, apezeke akukana machitachita a Akhristu tsopanoli amene amakana unsembe wa Khristu ndi kutiyimira kwake?

Ife tifunseko, kodi Khristu akuimira komanso kugwilira ntchito ndani kudzanja lamanja la Mulungu?

Kodi ndi chifukwa cha dziko lapansi?

Moonekeratu ayi ndithu, pakuti Iye akulankhula ku Yohane 18:9, “Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine, chifukwa ali anu.”

Ndipo amenewa ndi ndani?

Kodi anali Ayuda otsala?

Ayi ndithu; otsala amenewa adzaonekerabe mu zochitika.

Kodi nanga amenewa ndi ndani?

Okhulupilira, ana a Mulungu, Akhristu, amene akudutsa m’dziko lino la uchimo, ali nako kuthekera kwa kulephera ndi kuononga mayendedwe awo onse.

Imeneyi ndi mitu ya utumiki wa unsembe wa Khristu.

Iye anafa kuti iwo akayeretsedwe.

Iye akukhala ndi moyo kuti iwo akayeretsedwe.

Mwa imfa yake anathetsa kutsutsika kwathu, ndipo ndi moyo wake anatitsuka ife, kudzera mu machitachita a mau mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.

Ameneyu ndi yemwe anabwera mwa madzi ndi mwazi; osati mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwazi.”

Ife tili nako kuchotseredwa ndi kutsukidwa kwa machimo kudzera mwa Mpulumutsi wopachikidwa.

Kuyenda kophatikana kwa mwazi kochokera mu mthiti ya Khristu yobooledwa, amene anatifera ife.

Malemekezo onse apite kudzina lake!

Tili nazo zonse, mwa mphamvu ya imfa ya mtengo wapatali ya Khristu.

Kodi ndi funso lokhudza kutsutsika kwathu?

Inachotsedwa ndi mwazi wa chiombolo.

Kodi ndi funso lokhudza kulephera kwathu kwa tsiku ndi tsiku?

Ife tili naye wotiyimira ndi Atate – Wansembe Wamkulu ndi Mulungu.

Ngati munthu achimwa.” Iye sakunena kuti, “Ngati munthu alapa”

Nzosadabwitsa kuti pali ndipo pakuyenera kukhala kulapa ndi kudziweruza wekha.



Koma kodi zimakonzedwa bwanji?

Kodi zimachokera pati?

Zikuchokera apa: “Tili naye wotiyimira ndi Atate.”

Mapemphero ake amphamvu ndi omwe amagulira wochimwayo chisomo cha kulapa, kudziweruza yekha komanso kuvomereza.

Ndi zofunikira kwambiri kwa muwerengi wa Chikhristu kumvetsetsa za choonadi cha mfundo ya kuyimiridwa kapena unsembe wa Khristu.

Nthawi zina ife timaganiza kuti pamene talephera mu ntchito chinthu china chake chikuyenera kuchitika kumbali yathu kuti zinthu zikhalenso bwino pakati pa miyoyo yathu ndi Mulungu.

Ifetu timaiwala kuti, ngakhale pano tili ndi chikumbumtima cholephera – ngakhale chikumbumtima chathu chisanazindikire za mfundoyi – wotiyimira wathu wapita kale kwa Atate ndi zolakwazo; ndipo mu kupembedzera kwake ife tinagulilidwa chisomo cha kulapa, kuvomereza ndi kubwenzeretsedwa,

Ngati munthu aliyense achimwa, tili naye” – chiyani?

Mwazi wobwenzeretsedwa ku?



Ayi ndithu; taonani mosamalitsa zimene Mzimu Woyera akunena.

Ife tili naye wotiyimira ndi Atate, Yesu Khristu wolungama.”

Kodi ndi chifukwa chiyani Iye akunena kuti, “wolungama.”

Chifukwa chiyani sakunena wa chisomo, wa chifundo, wa chisoni?

Kodi Iye siali zonsezi?

Inde zoonadi ali zonsezi, koma pa zonsezi palibe chimene chimafotokozera za chikhalidwe chimene chaikidwa apa, pamene mtumwi wodalitsika akutiikira choonadi chotitonthoza, kuti mu zolakwitsa zathu zonse, machimo athu, komanso mu zolephera zathu, tili naye wotiyimira “wolungama” amene sanakhaleponso chiyambire wolungama wa Mulungu, Atate Woyera, cholinga kuti machimo athu asadzaonekerenso.

Iye akukhalabe ndi moyo kukatipembedzera ife;” komanso chifukwa chakuti amakhalabe ndi moyo, “Iye ali nako kuthekera kwa kupulumutsa koonjeza mlingo” – kufikira kumapeto – “iwo amene abwera kwa Mulungu mwa iye.”

Chilimbikitso cholimba ichi kwa anthu a Mulungu!

Komanso miyoyo yathu ndiyofunika kukhazikika mu chidziwitso ndi malingaliro a izi.

Ena mwa iwo kumeneko ali ndi malingaliro oipa a kuimikika kwenikweni kwa Mkhristu, chifukwa iwo samaona zimene Khristu anachita kwa iwo m’mbuyomu.

Anthu ena, mosemphanitsa ali ndi mbali imodzimodzi ya kaonedwe ka nyengo ya Mkhristu, kunena kuti samaona kufunikira kwathu pa zimene Khristu akutichitira ife pano.

Zonsezi zikuyenera kukonzedwa.

Mfundo yoyambayo ndi umbuli waukulu pa za ubwino wa chiombolo; mfundo yotsatirayo ndi umbuli pa za malo ndi machitidwe a wotiyimira.

Umenewu ndi ungwiro wa kayimidwe kathu, kamene Paulo akulankhula, “Monga iye ali, chomwecho ifenso tili mu dziko lapansi ili.”

Izi zikanakhala chomwechi, ifetu sitikanafunikira wansembe kapena wotiyimira.

Koma kenako, imeneyi ndiyo nyengo yathu, imene mtumwi akulankhula, “Ngati munthu aliyense achimwa.”

Zimenezi zikutsimikizira za kufunikira kwa Wotiyimira mopitilira.

Ndipo alemekezeke Mulungu, ifetu tili naye mopitilira; tili naye kukhalabe chifukwa cha ife.

Iye akukhala ndi kutumikira m’mwamba.

Iye ndi chilungamo chathu chokhalabe pamaso pa Mulungu.

Iye ali ndi moyo kukatipanga ife kukhala abwino kumwamba, ndiponso kutipanga ife kukhala abwino pamene talakwitsa padziko lapansi.

Iye ndi mlumikizi waumulungu komanso wosasungunuka pakati pa miyoyo yathu ndi Mulungu.

GAWO 4.

Pokhala ndi masamba atatu otsogozana a nkhani imeneyi, kufunitsitsa kuulula maziko a choonadi chachikulu cholumikizana ndi ntchito ya Khristu pa ife – ntchito yake kalelo, komanso ntchito yake mnyengo yino – kuombola kwake, komanso kutiyimira kwake; ife tidzafuna tsopano, mwa thandizo la chisomo cha Mzimu wa Mulungu, kupereka kwa muwerengi chinachake pa zimene Malemba amatiphunzitsa ife monga mwa gawo lachiwiri la nkhani yathu, yotchedwa,

KHRISTU NGATI CHIDA CHA MTIMA.

Chimakhala chinthu chodalitsika modwabwitsa kukwanitsa kulankhula kuti, “Ine ndapeza chida chimene chakwaniritsa mwangwiro mtima wanga – Ine ndapeza Khristu.”

Chida chimenechi ndi chomwe chimapereka kukwezedwa kwenikweni pamwamba padziko lapansi.

Chidachi chimapereka kwa ife ufulu wa kupeza zinthu zimene kwa mtima wosatembenuka umadzitengera okha.

Chida chimenechi chimapereka mpumulo wokhazikika.

Chimapereka kudekha ndi chete ku mzimu zimene dziko lapansi sizingamvetsetse.

Anthu a chipembedzo a dziko lapansi akhoza kuganiza kuti moyo wa Mkhristu weniweni ndi wochedwetsa, wogona, machitidwe wopusa kwambiri.

Iye akhoza kudabwa kuti munthu akhoza kukwanitsa bwanji kukhala moyo wopanda zimene iye akudzitchula zokoma ndi zosangalatsa; osaonera kanema – osaonera mpira – osapita ku madansi – osasewera njuga – osachita mipikisano yothamanga – osakhala nawo ku maphwando osiyanasiyana.

Kumukaniza zinthu ngati zimenezi munthu wosatembenuka mtima zikhoza kumutsogolera ku kukhumudwa kapena kuoneka ngati wopusa.

Komatu Mkhristu safuna zinthu zotere, ndipo sangakhale nazo.

Zimenezi zikhoza kukhala zotopetsa kwa iye.

Ifetu tikunena za Mkhristu weniweni, osati Mkhristu mu dzina koma mchoonadi.

Zachisoni! ambiri amanena kuti ndi Akhristu, ndipo amatenga maudindo apamwamba mu zochitika zawo, amene amapezeka akusanganizika mu zochitika za anthu a dziko lino lapansi.

Amene amapezeka pa mgonero wa Ambuye Tsiku la Ambuye ndipo tsiku Lolemba amapezeka akupita ku madansi.

Iwo angathe kupezeka akutenga nawo gawo mu zina zochitika mu ntchito ya Chikhristu Lamulungu, ndipo mkati mwa sabata mungathe kuwaona ali ku zochitika za uchimo za dziko lapansi.

Zimenezi ndi zachidziwikire kuti anthu otere palibe chimene amadziwa zokhudza Khristu monga chida cha mtima wawo.

Zoonadi ndi zokaikitsa kuti munthu amene ali ndi moyo wa umulungu wakumwamba m’moyo mwake akapeze zomusangalatsa mu zinthu zochitika m’dziko lapansi lopanda umulungu.

Mkhristu weniweni komanso wotsimikizika amachoka ku zinthu ngati zimenezi – amachokamo mwachangu.

Ndipo zimenezi, osati chifukwa cha kulakwika ndi kuipa kwake kokha – ngakhale kuti iye amazindikira kuti zimenezi ndi zolakwika komanso zoipa - koma chifukwa chakuti alibe chikhumbokhumbo cha izo, komanso chifukwa chakuti iye wapeza chinthu china chachikulu, chinthu chimene chimakhutitsa zokhumba zonse za chilengedwe chatsopano.

Kodi tikhoza kuganizira mngelo wakumwamba kukhala mu chisangalalo pa masewera, pa kanema kapena zokondweretsa za m’dziko lapansi?

Malingaliro amenewa ndi opanda pake zedi.

Zochitika zonsezi ndi zachikunja kwa mzika yakumwamba.

Kodi Mkhristu ndi ndani?

Iye ndi munthu wakumwamba; iye ndi wotenga nawo gawo mu chikhalidwe chakumwamba.

Iye ndi wakufa kudziko – wakufa ku tchimo – wamoyo kwa Mulungu.

Iye alibe mgwirizano wina ulionse ndi dziko lapansi.

Iye kwao ndi kumwamba.

Iye salinso wadziko lapansi koposa Khristu ndi Ambuye wake.

Kodi Khristu akhoza kutenga nawo gawo mu zosangalatsa, maphwando ndi zopusa za dziko lapansi?

Malingaliro oterewa ndi onyozetsa.

Nanga tsopano, zili motani ndi Mkhristu?

Kodi iye akuyenera kupezeka kumene Ambuye wake sangapezeke?

Kodi iye angathe kumatenga nawo gawo mu zinthu zimene iye akudziwa mu mtima mwake kuti ndi zosemphana ndi Khristu?

Kodi iye angathe kupita kumalo, kumadera ndi mu zochitika zimene iye akuvomereza kuti Mpulumutsi wake ndi Ambuye wake sangapezekeko?

Kodi iye akhoza kupita ndi kuyanjana ndi dziko lapansi limene limamuda Iye amene amawauza kuti ali nazo zinthu zonse?

Zingathe kuoneka kwa awerengi athu ena kuti talowa mkati kwambiri.

Ifetu tikuyenera kufunsa choncho, kodi tikuyenera kutenga gawo lanji?

Zoona tikuyenera kutenga gawo la Chikhristu, ngati ndife Akhristu.

Nanga ngati tikuyenera kutenga gawo la Chikhristu, kodi tingalidziwe bwanji gawo limeneli?

Motsimikizika tingathe kulidziwa kuchokera m’Chipangano Chatsopano.

Kodi chimatiphunzitsa chiyani?

Kodi chimakwanitsa kupereka chilolezo kuti Mkhristu azizisakaniza yekha, mwa mtundu wina ulionse ndi zosangalatsa ndi zinthu zakutha za dziko ili lapansi loipa?

Tiyeni timvere mau apamwamba a Ambuye wathu wodalitsika, ku Yohane 17.

Tiyeni timvere kuchokera pa milomo yake choonadi monga mwa cholowa chathu, nyengo yathu, komanso njira yathu m’dziko lino.

Iye akulankhula kwa Atate, “Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi linadana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali adziko lapansi monga Ine sindili wadziko lapansi. Patulani iwo mchoonadi; mau anu ndi choonadi. Monga momwe munandituma Ine kudziko lapansi.” Ndime 14-18.

Kodi ndi zotheka kuvomereza mlingo wapafupi wa kuzizindikira kuposera umene waikidwa patsogolo pathu m’mau amenewa?

Kawiri konse mu ndime yaifupi imeneyi, Ambuye wathu akunena kuti ife sitili adziko lapansi, monganso Iyenso siali wadziko lapansi.

Kodi Ambuye wathu wodalitsika ali nacho chiyani chakuchita ndi dziko lapansi? Palibe.

Dziko lapansi linamukana Iye, ndipo linamutaya Iye kunja.

Linamukhomera Iye pa mtanda wamanyazi, pakati pa achifwamba awiri.

Dziko lapansi limanama kwathunthu monga mwathupi pansi pa ulamuliro wa izi zonse, monga kuti ntchito ya kupachikidwa inachitika dzulo, mkatikati mwa kutsogola kwake ndi tanthauzo lake lalikulu mu zonse.

Palibe kulumikizana kwina kulikonse mu chikhalidwe pakati pa Khristu ndi dziko lapansi.

Inde, dziko lapansi lapakidwa ndi mwazi wa kuphedwa kwake, ndipo likuyenera kuyankha kwa Mulungu pa mlandu umenewu.

Zinthu zopambana zimenezi!

Kuganiziridwa kwa Mkhristu kwa mtengo wapatali!

Ife tikudutsa m’dziko lapansi limene linapachika Ambuye wathu, ndipo Iye akulengeza kuti sindife adziko lapansi, monganso Iye siali wadziko lapansi.

Kotero zotsatira zake ndi zakuti ngati ife tili m’chiyanjano china chilichonse ndi dziko lapansi, ndife Akhristu abodza.

Kodi mukhoza kuganiza motani za mkazi amene angakhale pansi, nkumaseka ndi kumachita nthabwala, ndi gulu la anthu limene linapha mwamuna wake?

Komabe zimenezi ndi zomwe amachita Akhristu a pakamwa chabe pamene asakanikirana ndi dziko ili lapansi loipa, ndi kudzipanga okha kukhala mbali imodzi ya dziko lapansi.

Mwina mukhoza kulankhula, “Kodi tichite chiyani? Tikuyenera kuchoka m’dziko lapansi?” Ayi ndithu.

Ambuye wathu akunena, “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.”

Kukhala m’dziko lapansi, koma osati wadziko lapansi, imeneyi ndi mfundo yeniyeni ya Mkhristu.

Kugwiritsa ntchito chithunzithunzi, Mkhristu m’dziko lapansi ali ngati munthu wosambira pansi pa madzi.

Iye amakhala mkatikati mwa zinthu zimene zikhoza kumuononga, akanakhala kuti siali wotetezedwa ndi machitidwe ake, ndi kulimbikitsidwa ndi malumikizidwe wosaphwanyika mu zochitika pamwamba pake.

Kodi nanga Mkhristu akuyenera kuchita chiyani m’dziko lapansi?

Kodi cholinga chake ndi chiyani?

Cholinga chake ndi ichi: Monga momwe munandituma Ine kudziko lapansi, inenso ndiwatuma kudziko lapansi.”

Komanso ku Yohane 20:21, “Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.”

Chimenechi ndicho cholinga cha Mkhristu.

Iye sakuyenera kudzitsekera yekha mkatikati mwa makoma a chipembedzo kapena lonjezano.

Chikhristu sichitengera kuti munthu alowe unsembe kapena usisitere.

Palibe chinthu chokhala ngati chimenechi.

Ife tinaitanidwa kukayenda mu chiyanjano chosiyanasiyana cha moyo, ndi kukachita mwa kuitanidwa mwa umulungu mwa ulemelero wa Mulungu.

Nkhani siyakuti tikuchita chiyani, koma momwe timachitira chinthucho.

Zonsezi zimatengera chida chimene chikulamulira mitima yathu.

Ngati Khristu ndi wolamulira komanso chida chokhala mu mtima, zonse zidzakhala bwino.

Ngati Iye siali choncho, palibe chabwino.

Anthu awiri akhoza kukhala limodzi pagome ndi kumadya; wina kudya kukhutitsa njala yake, winayo kudya ku ulemelero wa Mulungu – kudya cholinga cha kusunga thupi lake kukhala mu dongosolo la kutumikira bwino monga chida cha Mulungu, nyumba ya Mzimu Woyera, chida cha kutumikira Khristu.

Chomwecho mu zinthu zonse.

Ndi cholowa chathu chokoma kumuika Ambuye patsogolo pathu.

Iye ndiye chitsanzo chathu.

Monga Iye anatumidwa padziko lapansi, chomwecho ifenso.

Kodi Iye anabwera kudzachita chiyani?

Kudzalemekeza Mulungu.

Kodi Iye anakhala bwanji? Anakhala mwa Atate.

Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.” Yohane 6:57.

Zimenezi zikupangitsa zonse kukhala zophweka.

Khristu ndiye mlingo komanso muyeso wa zinthu zonse.

Sinkhaninso yokhudza kulondola ndi kulakwa molingana ndi malamulo a munthu.

Nkhani ndi yakuti choyenera ndi chiyani pa Khristu.

Kodi Iye achita ichi kapena icho?

Kodi Iye apita kuno kapena uko?

Iye anatisiyira ife chitsanzo kuti titsatire mapazi ake;” ndiponso motsimikiza, ife sitikuyenera kupita kumene sitingapeze mapazi ake odalitsika.

Ngati ife tingapite uko kapena kuno kukadzitsangalatsa tokha, ifetu sitikuyenda monga mwa mapazi ake, ndipo sitingayembekezere kusangalala mkupezeka kwake kodalitsika.

Muwerengi wa Chikhristu, pano pali chinsinsi chenicheni cha nkhani yonse.

Funso lalikulu ndi lakuti – kodi Khristu ndi chida changa chokhacho?

Kodi ine ndikukhala chifukwa cha ndani?

Kodi ndingathe kulankhula, “Moyo umene ndikukhala mu thupi, ndikukhala mwa chikhulupiliro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine?”

Chilichonse chotere ndicho chomuyenera Mkhristu.

Ndi chinthu chosakhala bwino kungokwaniritsidwa kuti tinapulumutsidwa, ndi kupitilira kukhalabe ndi dziko lapansi, ndi kukhala modzisangalatsa tokha ndi zolinga za ife eni – kuvomereza chipulumutso ngati chipatso cha kuzunzika ndi chifundo cha Khristu, ndi kukhala moyo wotalikana ndi Iye mwini.

Kodi tingaganize zotani kwa mwana amene amangosamala zinthu zabwino zimene atate wake akumuchitira koma iye osafuna kukhala chifupi ndi atate wakewo – inde, nasangalatsidwa kukhala pamodzi ndi alendo?

Ifetu tikhoza kumutaya mwana wotere koma nanga Mkhristu amachita zotere mochuluka bwanji, amene akuyenera kuchita kwamuyaya mu ntchito ya Khristu, komabe iye ali wosangalatsidwa kukhala motalikana ndi Munthu wake Wodalitsika, osati kusamalira za kukula kwa cholinga chake – kutukula ulemelero wake!

GAWO 5.

Ngati muwerengi wapatsidwa kuthekera, mwa chisomo, kuchita mwa iye yekha pa zimene zadutsa m’malingaliro athu mu zolembedwa zimenezi, iye akakhala ndi yankho labwino pa kusakhazikika konse kwa chikumbumtima komanso kusoweka mtendere konse kwa mtima.

Ntchito ya Khristu, ikanakhala kuti yakhazikika pa chikhulupiliro chopanda luso, chokakamiza, chokhala ndi cholinga chodalitsika, kukumana ndi Munthu Khristu, ngati Iye akakhazikika ndi diso limodzi, akhoza kukumana mwangwiro ndi Khristu.

Ngati ife sitili mu chisangalalo cha mtendere wa chikumbumtima, chifukwa chikhoza kukhala kuti ifeyo sitikupeza mpumulo pa ntchito yotsirizika ya Khristu; ndipo ngati mtima siuli m’malo, zimangosonyezera poyera kuti ifeyo sitikukhutitsidwa ndi Khristu mwini.

Komabe, zachisoni! kuti pali ochepa, ngakhale pakati pa anthu okondeka a Ambuye, amene amadziwapo chimodzi kapena china.

Zithu zovuta kupeza munthu amene ali mu chisangalalo chenicheni cha mtendere wa chikumbumtima komanso mpumulo wa mu mtima! Kulankhula mowomba mkota, Akhristu siali ochepa monga mwa nyengo ya oyera mtima a m’Chipangano Chakale.



Iwo samadziwa kudalitsika kwa chiombolo chokwaniritsidwa.

Iwo siali mu chisangalalo cha chikumbumtima choyera.

Iwo sangasendeze chifupi ndi mtima weniweni, wa chitsimikizo cha chikhulupiliro, kukhala nawo mtima kuwazidwa mu chikumbumtima choipa, komanso thupi lotsukidwa ndi madzi woyera.

Iwo samaphunzira choonadi chachikulu cha Mzimu Woyera wokhalira mwa iwo, kuwathandizira kulira, “Abba, Atate.”

Monga mwa chizolowezi chawo iwo ali pansi pa lamulo.

Iwo sanalowepo mkudalitsika kwakuya kokhala pansi pa ulamuliro wa chisomo.

Iwo ali ndi moyo.

Nzosatheka kukaikira zimenezi.

Iwo amakonda zinthu za umulungu.

Kulawa kwawo, khalidwe lawo, machitidwe awo, inde ntchito zawo, mikangano yawo, zisangalalo zawo, kukayika, ndi mantha zonsezi zimatsimikizira kupezeka kwa moyo wa umulungu.

Iwo mwanjira ina, analekanitsidwa kudziko lapansi, komatu kulekanitsidwa kwawo kuli kowawa osati kwabwino.

Zimenezi ndi zambiri chifukwa iwo amaona kutha kwa dziko lapansi, komanso kusakwaniritsa kwake pa mitima yawo, osati chifukwa anapeza chida mwa Khristu.

Iwo anataya chilakolako chawo pa zinthu za dziko lapansi, koma sanapeze malo awo komanso gawo lawo mwa Mwana wa Mulungu kumene Iye tsopano ali kudzanja lamanja la Mulungu.

Zinthu za dziko lapansi sizingawakwaniritse iwo, ndipo iwo siali mu chisangalalo cha kuima kwawo koyenera kwa kumwamba, chida chawo, ndi chiyembekezo chawo; komabe iwo ali mu nyengo yosakhala bwino; iwo alibe chitsimikizo, alibe mpumulo, alibe cholinga pa zochita; iwo siali osangalala; iwo sadziwa chenicheni chimene iwo akutenga; iwo siali kanthu aka kapena kena.

Kodi zili chonchi ndi muwerengi?

Ife tikukhulupilira kuti sizili chonchi.

Ife tili ndi chikhulupiliro kuti iye ndi m’modzi wa iwo, kudzera mu chisomo chopanda malire.

Dziwani zinthu zimene zimaperekedwa ndi Mulungu kwa iwo mwaulere,” amene akudziwa kuti achoka ku imfa kupita ku moyo – kuti ali ndi moyo wosatha; amene amasangalala ndi umboni wa mtengo wapatali wa Mzimu; iwo amene amazindikira kulumikizana kwawo ndi Mutu woukitsidwa ndi wokwezedwa m’mwamba, amene alumikizana pamodzi ndi Mzimu Woyera amene akhalira mwa iwo; amene apeza chida chawo mwa Munthu Wolemekezeka amene anamaliza ntchito ndiye chiyambi cha umulungu chamuyaya cha chipulumutso chawo ndi mtendere; ndipo iwo akuyang’ana mwachidwi nyengo yodalitsika pamene Yesu adzabwera kuwalandira iwo pa Iye yekha, kuti kumene Iye ali akakhalenso iwo, kuti asatulukenso kunja kwamuyaya.

Chimenechi ndicho Chikhristu.



Palibenso wina amene akuyenera dzinali.

Chikhristu chimaima mosiyana ndi machitidwe a chipembedzo cha masiku ano, chimene chimakhala Chiyuda chenicheni mbali inayi, komanso Chikhristu chenicheni mbali inayi, komatu ameneyu ndi kasakaniza woipa, wokhala nazo zochitika kuchokera ku mbali zonse, zimene wosatembenuka mtima angathe kudzitengera ndi kumachita, chifukwa zimagwirizana ndi zokhumba za thupi, ndipo iwo amavomerezedwa kusangalala ndi zakutha za dziko lapansi molingana ndi kukhutitsidwa kwa mitima yawo.

Mdani wamkulu wa Khristu komanso wa miyoyo yathu wapambana pakukonza mchitidwe woipa wa chipembedzo, chiyuda-theka, Chikhristu-theka, kuziphatikiza, mwanjira ya luso kwambiri, za dziko lapansi ndi thupi, kuphatikizirapo malemba cholinga kuti awononge mphamvu ya kuipa kwake, ndi kupsinjiriza tanthauzo lake.



Mu ziyangoyango za machitidwe amenewa miyoyo yakodwa mopanda chiyembekezo.

Anthu osatembenuka mtima akuputsitsidwa mu malingaliro amenewa kuti iwo ndi Akhristu abwino ndithu, ndipo akupita kumwamba.

Ndipo mbali inayi, anthu okondedwa a Ambuye akuberedwa malo awo owayenera komanso zolowa zawo, ndipo amakokedwa pansi ndi zokopa za mumdima ndi zofooketsa za chipembedzo zimene zimawazungulira ndi kuwatsamwitsa iwo.

Ifetu tikukhulupilira kuti izi zili mozungulilidwa ndi chilankhulo cha umunthu kukhazikitsa zotsatira zodabwitsa za kusakanikirana kwa anthu a Mulungu ndi anthu a dziko lapansi ndi cholinga cha ndondomeko imodzi ya kupembedza ndi chikhulupiliro pa chipembedzo.

Chotsatira chake cha anthu a dziko lapansi ndicho kuwaphimba kumaso ku chikhalidwe cha ulemelero cha Chikhristu monga chakhazikitsidwira mu masamba a m’Chipangano Chatsopano; ndipo zimenezi ku mlingo wotere, kuti ngati munthu ayesera kufunyulula ma ulemelero amenewa ku malingaliro awo, amatengedwa ngati munthu wa masomphenya osokoneza, kapenanso munthu wokhala ndi chiphunzitso choipa.

Zotsatira zake pa iwo ndizo kupusitsidwa monga mwa nyengo yawo yeniyeni, chikhalidwe chawo ndi mathero awo.

Mbali zonse zimabwereza njira zofanana, kuloweza chikhulupiliro chofanana, kunena mapemphero ofanana, ma membala a dera limodzi kutenga ma saklamenti ofanana, amene ali afupi, olembedwa mwa luso, mwa chipembedzo, mwa uzimu.

Zinalembedwa kale pakuyankha zimenezi, kuti Ambuye, mwa kulingalira kwake kodabwitsa ku Mateyu 13, akuphunzitsa kuti tirigu ndi namsongole zikulire limodzi.

Inde; koma zikulire kuti?

Mu mpingo?

Ayi ndithu; koma “kumunda;” ndipo Iye akutiuza kuti “munda ndiye dziko lapansi.”

Kusakaniza zinthu zimenezi ndiko kunyazitsa mlingo wa chikhristu chonse, komanso kuchotsa mwambo onse wa umulungu mu mpingo.

Ndiko kuika chiphunzitso cha Ambuye wathu ku Mateyu 13 kutsutsana ndi chiphunzitso cha Mzimu Woyera ku 1 Akorinto 5.

Komabe sitikuyenera kupitilira ndi mutu umenewu pano.

Zinthuzi ndi zofunikira kwambiri komanso zazikulu kuti sitingathe kuzikambirana mu nkhani ya chidule ngati imene tikukamba panoyi.

Ifetu tidzakambirana bwino, mwatchutchutchu mu nyengo ina ya mtsogolomu.

Kunena kuti zimafunika kuganizira mofatsa kwa muwerengi wa Chikhristu ifetu pamenepa timatsimikizika; kuganizira, monga momwe zichitikira, mwa ulemelero wa Khristu mwa cholinga chenicheni cha anthu ake, mwa kupambana kwa uthenga, mwa chilungamo cha umboni ndi utumiki wa Chikhristu, zikhoza kukhala zovuta kuonjeza maonedwe a kufunika kwake.

Koma tikuyenera kusiya kaye pakali pano, pakutseka kaye nkhaniyi ndi chifanizo chapafupi cha gawo lachitatu ndi gawo lomaliza la mutu wathu, wotchedwa,

MAU A KHRISTU MONGA MLOZO WOKWANIRA PANJIRA YATHU.

Ngati ntchito ya Khristu imakwanira pa chikumbumtima, ngati Munthu wodalitsika amakwanira mu mtima, motsimikizika, Mau ake a mtengo wapatali amakwaniranso panjira yathu.

Tikhoza kunena mwa kulimbika konse, kuti ife tili ndi mulu wa malemba a umulungu amene tikhoza kuwafuna, osati kungofikira kufunikira konse kwa njira yathu patokha, komanso kufunikira kosiyanasiyana kwa mpingo wa Mulungu, mu mndandanda wa mbiri yake padziko lino lapansi.

Ife timadziwa kuti pakuchita zimenezi timadzipereka tokha poyera kukunyozedwa ndi kutsutsidwa, ku madera ochuluka osati dera limodzi.

Ifetu mbali inayi tidzakumana ndi oimira chikhalidwe, ndipo mbali inayi iwo amene amatsutsana pa ukulu wa malingaliro a munthu komanso cholinga chake.

Koma zimenezi zimatipatsadi nkhawa yochepa.

Ife timalemekeza chikhalidwe cha anthu, pena atate, abale, madokotala, ngati zoperekedwa monga mwa ulamuliro, monga fumbi lochepa pa mlingo; monganso mwa zolinga za umunthu, zingathe kufanizidwa ndi mleme kuuluka dzuwa likuwala, kusokonezeka ndi kuwala, mwakhungu kumaziombetsa yekha ku zinthu zimene iye sakudziona.

Chimakhala chisangalalo kwa mtima wa Mkhristu kuchoka ku makhalidwe ndi ziphunzitso zotsutsana za anthu ndi kupita ku kuwala kwa malemba woyera; ndipo akakumana ndi malingaliro a chipembedzo, anzeru zawo, anthu okaikakaika, kukagwada pansi kwa chikhalidwe chake chonse ku ulamuliro ndi mphamvu ya malemba woyera.

Iye amayamikira ndi kuzindikira mu Mau a Mulungu mlingo wokhawo wapamwamba wa chiphunzitso, chikhalidwe ndi zinthu zonse.

Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha mchilungamo; kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.

Kodi tifunikanso chiyani?

Palibe.

Ngati malemba angamupangitse mwana kukhala “wanzeru ku chipulumutso,” ndipo akhoza kupangitsanso munthu kukhala “wangwiro” komanso kumukonza iye “ku ntchito zonse zabwino,” nanga tifuniranji chikhalidwe cha umunthu kapena malingaliro a umunthu?

Ngati Mulungu watilembera ife buku, ngati Iye anavomereza kutipatsa ife vumbulutso la malingaliro ake, pa zonse zimene tikuyenera kuzidziwa, kuganiza, kumva, kukhulupilira ndi kuchita, kodi tikuyenera kubwerera kwa munthu mzathu wosakhalitsa – kaya akhale wa matsenga kapena wanzeru – kuti atithandize ife?

Malingaliro amenewa akuyenera kukhala kutali!

Kapenanso tikuyenera kubwerera kwa munthu mnzathu kukaonjezera zinthu zina pa imfa yokwanira ya Khristu, cholinga kuti zikaoneke zokwanira pa chikumbumtima chathu, kapena kuika ubwino wina mwa Munthu Khristu, cholinga kuti Iye apatsidwe chida cha mtima, monga kudzitengera tokha ku chikhalidwe cha umunthu kapena zifukwa za umunthu kupereka ubwino mu vumbulutso la umulungu.

Malemekezo ndi matamando onse zipite kwa Mulungu wathu, zikuyenera kukhala choncho.

Iye anatipatsa ife Mwana wake wokondedwa chimene tikufunikira pa chikumbumtima, mu mtima, munjira – pa nthawi yake, ndi nyengo zake zonse zosintha – kwamuyaya, ndi nyengo zake zosawerengeka.

Ifetu tikhoza kulankhula, “Inu, Khristu, ndinu amene ife tikufuna; koposa mwa Inu timapeza zonse.”

Mulibe ndipo simudzakhala kusowa mwa Khristu wa Mulungu.

Kuombola kwake ndi kutiyimira kwake kukwaniritse ufulu onse wakuchitika mu chikumbumtima.

Chikhalidwe cha ulemelero, kukopa kwa mphamvu, kwa Umunthu wake wa umulungu kukwaniritse kukhumba kwakukulu kwa mtima.

Komanso kusiyana kwa vumbulutso lake – buku la ulere lokhala nalo mkati mwake zimene ife tingafune, kuchokera poyambira pathu kukafika pa cholinga cha ntchito yathu ya Chikhristu.

Muwerengi wa chikhristu, kodi zinthu sizili choncho?

Kodi simungathe, kuchokera mkatikati mwa chikhalidwe chanu chokonzedwa, kukhala ndi choonadi cha iwo?

Ngati ndi choncho, kodi inu mukupuma, mwachete mu ntchito ya Khristu?

Kodi inu mukusangalala mu Umunthu wake?

Kodi inu mukudzipereka mu zinthu zonse ku ulamuliro wa Mau ake?

Mulungu wapereka ndipo zikhalenso chomwecho ndi inu, komanso kwa onse amene anenera Dzina lake!



Pakhale umboni wathunthu, omveka bwino, ndi wokhazikika ku “Kukwaniritsa konse kwa Khristu,” kufikira “tsiku limenelo!”