Kodi mumapemphera kwa ndani?



Kufotokozera



Cholinga cha nkhani yotsatirayi ndi kutetezera dongosolo la Baibulo pa kumulankhula Mwana wa Mulungu wodalitsika mu pemphero ndi kulambira.

Ngakhale kuti dongosolo limeneli limakanidwa ndi zipembedzo zina, zitionetsera kuti mu Chipangano Chatsopano pemphero silimaperekedwa kwa Mulungu Atate yekha koma limaperekedwanso kwa Ambuye Yesu Khristu.

Umboni wothandizira utengedwa kuchokera mu mbiri komanso mu nyimbo.

Pemphero likuyenera kupita kwa Atate kapena kwa Mwana monga Ambuye, koma palibe lamulo lochokera m’Malembo lokhudza pemphero lopita kwa Mzimu Woyera.



Iye ndiye muunikiri wa umulungu.

Iye amabweretsa ulemerero kwa Mwana (Yohane 16:13-14) monga Mwana aonetsera Atate (Yohane 1:18).

Mwachidziwikire, pemphero limapita kwa Mulungu Atate (Agalatiya 4:6) mudzina la Ambuye Yesu Khristu (Yohane 14:13), koma zimenezi sitizikamba pano.

Mutu wathu ndi pemphero kwa Khristu monga zikuonekera mu ma Uthenga Abwino, mu Machitidwe, ndi mu Makalata, komanso mu mbiri ya mpingo ndi nyimbo zake.

PEMPHERO KWA KHRISTU MU MAUTHENGA ABWINO

Ophunzira a Yesu amamulankhula Iye, kuitanira pa Iye ndi kupemphera kwa Iye mu nthawi ya kuyenda kwake padziko lapansi.

Mateyu, Marko, Luka ndi Yohane ali odzadza ndi zitsanzo zodabwitsa za ophunzira khumi ndi awiri komanso ena amene amaitanira pa Ambuye Yesu.

Chofunika kuzindikira ndi chakuti Iye samaitanidwa mwachindunji monga ‘Yesu.’

Iye amaitanidwa Ambuye kapena Mphunzitsi.



Onani zitsanzo zotsatirazi:

1) ‘Ndipo pamene Iye (Yesu) atalowa m’ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye. Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali mtulo. Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tili kutayika’ (Mateyu 8:23-25).

Iwo anazindikira za kuthekera kwake kuwapulumutsa m’mavuto.

Mauwa akugwirizana ndi mfundo ya mu Chipangano Chakale:

‘aliyense adzaitana padzina la Yehova adzapulumutsidwa’ (Yoweli 2:32).

Kumeneku kunalidi kulira kwa chipulumutso.

Iye anamva ndi kuyankha pemphero lawo.

Iye ali ‘yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthawi zonse’ (Ahebri 13:8).

Iye angathe kutipulumutsa ife lero ngati tiitanira pa Iye.

2) Kuvomerezedwa kwa machimo kumachitika kwa Khristu.

Zimenezi sizikungopereka umboni wa umulungu wake, koma zikuonetseranso mfundo yakuti Khristu analankhulidwa.

Pachiyambi pa utumiki wa Ambuye pa wanthu, Petro anavomereza za choonadi cha uchimo wake.

Anagwa pansi pa mabondo ake a Yesu, nanena, ‘Muchoke kwa ine Ambuye, chifukwa ndine wochimwa’ (Luka 5:8).

3) Pa phiri la kusandulizika, pamene Ambuye anasandulika pamaso pa ophunzira atatu okonderedwa komanso oyera mtima awiri a m’Chipangano Chakale, Mose ndi Eliya, Petro anayankha ndipo anati kwa Yesu,

‘Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano …… (Mat. 17:4)

Ophunzirawa anazindikira kuti Ambuye Yesu sanali munthu wamba.

Anayang’ana pa iye monga Mesiya (Khristu kapena Wodzodzedwa wa Mulungu), amene akuonekera tsopano mu nyengo ya ulemerero pamaso pawo.

Pamene tli nacho chikumbumtima cha kupezeka kwa Ambuye ifenso tingathe kulengeza kuyamika kwathu chifukwa cha mwayi umenewu: ‘Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano.’

4) Pa mfundo ina yosiyana, panali munthu amene anapachikidwa ndi Yesu.

Ife sitikudziwa zambiri za iyeyu, kupatula pa mfundo yokhayo kuti anali kabwerebwere, wakuba.

Iye pamodzi ndi munthu wina wopachikidwa atatha kumnyoza Ambuye Yesu, anabwerera ku malingaliro ake.

Iye anati kwa Yesu, ‘Ambuye, ndikumbukireni m’mene mulowa ufumu wanu.’

Mayankhidwe ake ndi achifumu: ‘indetu (indetu) ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m’Paradaiso’ (Luka 23:42-43).

Tikuonanso kukwaniritsidwa kwa lonjezano lakuti onse oitanira padzina la Ambuye adzapulumutsidwa.

Chilimbikitso chotani chimenechi, kuti ngakhale mapemphero a anthu otsala pang’ono kufa operekedwa m’chikhulupiriro amamvedwa ndi kuyankhidwa.

Kuchokera mu mfundo zochepazi tikutha kuona mapemphero amalankhulidwa kwa Ambuye Yesu m’mauthenga abwino.

Iye anali Mulungu ‘amene anaonekera mthupi’ (1 Tim. 3:16), ngakhale anadzichepetsa padziko lapansi pano.

Komanso tikuona kuti Iye sanangomva kokha mapempherowo koma anawayankha.

PEMPHERO KWA KHRISTU MU MACHITIDWE

Atakwera kumwamba kwa Atate kudzanja lamanja, Ambuye Yesu Khristu anatumiza Mzimu Woyera, lonjezano la Atate (Mach. 2).

Buku la Machitidwe limafotokozedwa kawirikawiri ngati ntchito za Mzimu Woyera

Munthu wa umulunguyu akuoneka akuyenda, akuyankhula komanso kutsogolera m’buku lonseli.

Komatu, palibe chitsanzo cha wophunzira akupemphera kwa Iye ngakhale kuti Iye ndi munthu wa umulungu.

Komabe, pali zitsazo zingapo za akhristu oyambilira kupemphera kwa Khristu wouka ndi wokwezedwa.

Wina analiyesa dzina la ‘Ambuye Yesu’ monga dzina losonkhaniranapo.

Zimenezi zili chomwechi chifukwa Machitidwe Atumwi akuonetsera kukambitsana pakati pa thupi (wokhulupirira) padziko lapansi komanso Mutu (Yesu Khristu) kumwamba, ndipo tikupeza kuti Iye akutchulidwa monga Ambuye Yesu kapena Ambuye osati Khristu Yesu kapena Yesu Khristu.

Stefano, m’modzi wa atumiki osankhika mumpingo wa ku Yerusalemu (Mach. 6:5), anali chida cha mazunzo. Atamaliza kupereka uthenga molimba mtima ku bwalo la akulu, iye anaponyedwa miyala mpaka kufa, kukhala munthu woyamba kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro (Mach. 7:58-60).

Iye anaitanira pa Mulungu mu pemphero nanena, ‘Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.’

Ambuye tsopano anali kumwamba pamene Stefano akuonetsera nkulankhula kwake, ‘Taonani, ndipenya m’Mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu ali kuimira pa dzanja lamanja la Mulungu’ (Mach. 7:56).

Kenako, akuponyedwabe miyala, iye anagwada (kupemphera kotani kumeneku!1) ndipo analira ndi mau okweza, ‘Ambuye musawaikire iwo tchimo ili.’



Kupemphera chogwada ndiwo mapempheredwe odziwika bwino molingana ndi Malemba. Kuimirira popemphera kunalembedwanso, koma kupemphera chokhala kunalembedwa kamodzi kokha (ndi mfumu Davide). Ulemu ndi ofunika. Chikhalidwe cha chibwana choika manja m’matumba popemphera pamaso pa Mulungu ndi chosayenera.

Iye anakwaniritsa chiphunzitso cha Ambuye wake wodalitsika: ‘Kondanani nawo adani anu ndi kupempherera iwo akuzunza inu’ (Mat. 5:44).

Palibe chasinthapo kuchokera mu nthawi ya ophunzira m’buku la Machitidwe Atumwi; munyengo ya zoopsa kapena ya zosowa, m’Khristu amalira, ‘Ambuye Yesu.’

  1. Pamene Khristu woukitsidwa kwa akufa akumulankhula Saulo (amene pambuyo pake akutchedwa Paulo), ‘Saulo, Saulo undilondalonderanji?’ iye akuyankha mwa pemphero la chindunji kwa Khristu wokwezedwa, ‘Ndinu yani Ambuye?’ komanso ‘ndidzachita chiyani Ambuye?’ (Machitidwe 9:5-6 komanso 22:10).



Iye amapemphera kuti adziwe chifuniro cha Mulungu.

Iye ndi munthu womvera; pamaso pa Mulungu wake wamkulu.

Yankho lake silikufanana ndi la Petro pokhudza za mtumwi Yohane, ‘Ambuye: koma nanga munthu uyu (Yohane)? (Yohane 21:21).

Iye sali otanganidwa ndi chifuniro cha Mulungu kwa ena koma kwa iye yekha.

Pano pali munthu wopemphera.

Pemphero lake likulunjika kwa Ambuye Yesu Khristu.

PEMPHERO KWA KHRISTU M’MAKALATA

7) Chipulumutso, makamaka chilungamitso mwa chikhulupiliro chokha, ndiwo mutu wa kalata ya mphamvu ya Paulo kwa Aroma.

Atatha kulengeza za chionongeko cha munthu kudzera mu tchimo, komanso njira yothetsera tchimolo mu uthenga wabwino, mtumwi akukhadzikitsa kufunikira kwa kuvomereza Yesu ngati Ambuye.

Iye akufananitsa ndi ndime ya m’Chipangano Chakale yomwe taiona kale, ‘pakuti, amene aliyense adzaitana padzina la Ambuye adzapulumuka’ (Aroma 10:13).

Pakuti Ambuye Yesu akuonetsedwa bwino m’Chipangano Chatsopano ngati Yehova wa m’Chipangano Chakale, palibe vuto kupemphera mwachindunji kwa Iye komanso kwa Atate.

Makamaka, pemphero lopita kwa Iye limaonetsera choonadi chenicheni cha umulungu wake.

8) Paulo anatunduzidwa ndi mazunzo a kuthupi pamene amatumikira Ambuye Yesu, chimene iye anachitchula ngati ‘munga mthupi, ndiye mngelo wa Satana’ (2 Akor. 12:7).

Iye anapempherera mamasulidwe monganso anthu ochuluka anapempherera kulowererapo kwa umulungu ndi kulanditsidwa kwake.

Iwo anapeza mamasulidwe a Ambuye koma kupempha kwa Paulo kunakanidwa ngakhale kuti iye anapemphera katatu konse.

Iye anapemphera, osati kwa Mulungu Atate, koma kwa Ambuye Yesu Khristu, ndipo akulemba zomwe anakumana nazo:

‘za ichi ndinapemphera kwa Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine’ (2 Akor. 12:8)

Ambuye analankhula, ‘ayi’ komanso anaonjezera, ‘chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko’ (2 Akor. 12:9).

Mu Akorinto Woyamba, ‘kalata ya Umbuye Wake’, pamene mau akuti ‘Ambuye’ (m’chigiriki: Kyrios, pamenepa kutanthauza; mbuye wamphamvu) akugwiritsiwa ntchito kokwanira 69, Paulo akulengeza kuti mpingo ukhale ndi anthu opemphera mwachindunji kwa Ambuye Yesu. Taonani mfundo ya mu chaputala 1 ndime 2: ‘………. kwa mpingo wa Mulungu wakukhala m’Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m’malo monse, ndiye wao ndi wathu;

Kalatayi ikulembedwera kwa mpingo wa Mulungu, osati kwa mkhristu m’modzi payekha payekha, komanso kwa okhulupirira ena onse mderalo;

amene akutchulidwa kumalo ena, a pa banja la chikhulupiriro (Agalatiya 6:10). Mutu wake ndi dongosolo la mu mpingo, ndipo akulembera kwa iwo akutsutsana naye pa nkhani ya kuphimba kumutu:

‘Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Eklesia wa Mulungu’ (1 Akor. 11:16) chimodzi mwa zizindikiro za mpingo wa Mulungu ndi ichi: anthu ake amaitanira pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.

Limeneli sipemphero chabe mudzina lake, koma kuitanira padzina lodalitsikalo; ndiko kulankhula naye mwachindunji.

Mu Timoteo Wachiwiri Paulo akufotokoza za nthawi ya kuchoka mu choonadi ndi kulephera, koma akulemba kuti adzakhalapobe ena akuitanira pa dzina la Ambuye. Iye akumulimbikitsa Timoteo: ‘Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera’ (2 Tim. 2:22)

Mu tsiku limene nyumba ya Mulungu (mkumano wa Mulungu), imene ikufotokozedwa ku 1 Timoteo 3:5 ngati mzati ndi mchilikizo wa choonadi, ikufalikira kuzungulira ‘nyumba yaikulu’, imene ku 2 Timoteo 2:20-21 ikufotokozera monga ya bodza, alipo amene amafunitsitsa kuitanira pa Ambuye ndi mtima woona (chitsanzo; amene ali ndi zolinga zosasakaniza)

Ndi zochititsa chifundo kuona kuti anthu ambiri samapemphera kwa Mwana wa Mulungu.

Ndipo ndi zochititsa chifundo kwambiri kuona kuti anthu ena amaletsa amzawo kuchita zimenezi kudzera m’chiphunzitso chawo!

  1. M’buku la chivumbulutso pemphero lomaliza lenileni mu Baibulo likuperekedwa kwa Mwana wa Mulungu: ‘Idzani Ambuye Yesu’ (Chiv. 22:20).

Chinthu cha mtengo wapatali kuti iwo omudziwa Iye aitanire pa Iye za kubweranso kwake kuti akadziwe kupezeka kwake mu chidzalo chake chonse.

Zimenezi zikuonetsera zikhumbokhumbo zawo kukhala chifupi ndi zimene zimakopa mitima yawo.

PEMPHERO KWA KHRISTU MU MBIRIZitsanzo za mbiri zotsatirazi zinatengedwa kuchokera kwa Ambrose, amene anali mtsogoleri wa mpingo mzaka za m’ma 4 century; John Owen munthu wodziwika amene anaphunzira za ubusa mzaka za m’ma 17 century; komanso John Darby, mlembi wa phindu pakati pa ‘Abale a ku Plymouth’ mzaka za m’ma 19 century.

Alembi amenewa akuonetsera njira ya m’Baibulo ya kapempheredwe ndi malambiro kwa Mulungu Mwana.

Zimenezi zionetsera poyera kuti pemphero lakhala likuperekedwa kwa Ambuye Yesu m’magawo onse a mbiri ya mu mpingo.



  1. Nyimbo ya Ambrose, mzaka za m’ma 4 century



Khristu, ndinu Mfumu ya ulemerero

Ndinu Mwana wamuyaya wa Atate.

Munadzitengera nokha kukapulumutsa munthu,

Inu simunapeputsa mimba ya Namwali.

Mutagonjetsa mbola ya imfa, Inu munatsegula

Ufumu Wakumwamba kwa okhulupirira onse.

Inu munakhala kudzanja lamanja la Mulungu mu ulemerero wa Atate

Tikukhulupirira kuti mudzabwera kudzakhala Oweruza wathu

Kotero, tikukupemphani kuti muthandize akapolo anu amene

Munawawombola ndi mwazi wanu wa mtengo wapatali.

Muwalole kuti awerengedwe pamodzi ndi oyera mtima mu ulemerero wanu wamuyaya2





Nyimbo ya (kwa Inu Mulungu) ndi nyimbo ya utatu wa ulemerero wa Mulungu ya m’ma 4 century

Gawo lake loyambilira likukamba za Mulungu Atate, koma gawo lachiwiri ndi chisonyezo cha ulemerero wa kulambira kupita kwa Mulungu Mwana, kulengeza mutu wa uzimu, chiombolo, chiukitso komanso kukwera.

Gawo lachitatu sakukamba za Mzimu, koma ndiyo ndondomeko ya malemekezo kupita kwa Mulungu yochokera ku Masalmo.b) John Owen, m’modzi mwa anthu a mpatuko mzaka za m’ma (1616 - 1683) kuchokera

m’buku lake la “Umunthu wa Khristu”.3‘Pemphero ndi nthambi yachiwiri yodziwikiratu ya ulemu wa umulungu – ulemu umene ukuyenera kuperekedwa kwa Mwana, monganso kwa Atate.

Amenewa ndi machitachita oyamba a chikhulupiliro cha umulungu-kupuma kwa moyo wauzimu... [ndiko]

Chiyambi cha machitidwe a umulungu wonse ndi kuchita bwino kwa iye amene timchimwira [kwa iye amene timapemphera]

Komabe Mtumwi akuufotokozera mpingo, kapena okhulupirira, ndipo akuwasiyanitsa iwo ndi ena onse, pakagwiridwe ka ntchito imeneyi (1 Akor. 1:2), ‘ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima pamodzi ndi onse’

Kuitanira padzina la Ambuye Yesu zimaonetsera ulemu wapadera munjira ya kulambira mwa uzimu.

Ayuda amaitanira padzina la Mulungu.

Anthu ena onse amaitanira pa maina a milungu yawo.

Pamenepa ndi pomwe mpingo umasiyanirana ndi onsewa – mpingo umaitanira padzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.’

‘Ndipo zolinga sizisowekapo.

Zonse zimene Ambuye watichitira, komanso mfundo zonse za chikondi, chisomo, chifundo ndi mphamvu, kuchokera ku zimene wachita zikupitirira ku chilengedwe cha umulunguchi……..

Kuchotsa ntchito imeneyi, komanso ubwino wapadera wa chipembedzo cha Chikhristu kwaonongedwa. ……….ena sangavomereze kuti ndi koyenera kwa ife kuitanira pa Khristu mwini….

Iwo amene amakana umulungu wa Khristu amavomereza kuti ndi kololedwa kwa ife kuitanira pa Khristu; koma amakana kuti ndi ntchito yathu nthawi iliyonse kuchita zimenezi.

Koma pamene akunena kuti sintchito yathu, koma mu mfundo zawo sizingakhale zololedwa.

Kukana umunthu wake wa umulungu, iwo amamusiya kusakhala chida choyenera cha pemphero.’

‘Chitsanzo chili pano, molingana ndi mayesero, komanso kupsinjika zikuyankhidwa, ndipo zikupezeka mwa Mtumwi Paulo.

Iye anali ndi “munga mthupi,” “mngelo wa Satana kumtundudza” iye.

“Za ichi anapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa iye” 2 Akor. 12:7, 8.

Iye anadzipereka yekha m’pemphero kuti munga ichoke, ndipo anachita izi mobwereza.

Anali Ambuye – amene ali Ambuye Yesu Khristu – amene iye anaperekako pemphero lake.‘mu pemphero kwa Khristu, timapereka ulemu kwa Mwana, monganso timapereka ulemu kwa Atate.’

C) Kuchokera ku malemba a John Nelson Darby (1800-1882)

Kundiuza kuti ndisalambire Khristu: mumandichotsera Khristu yekhayo amene ndimudziwa.

Ine ndilibe wina kupatula m’modzi amene ndimamulemekeza ndi kumulambira ndi mtima wa chiyamiko umene uyenera kupita kwa Iye.

Chithunzithunzi cha Yohane 16:27 chikupereka kudalira mwa Atate, kusiyana ndi mzimu wa Malita, ndime 11:22.

Pano Ambuye akulankhula, “Sindinanena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate: pakuti Atate yekha akonda inu” (ndime 26).

Popitiliza, pamenepa sakukamba za kulambira konse ayi, sakuyenera kufunsa kanthu kena kalikonse (eroto), koma akuyenera kumupempha (aitero) Atate mdzina lake.

Koma angelo onse a Mulungu akuyenera kumulambira Iye, bondo lililonse kugwadira Iye. Komanso kuonjezerapo: kuitanira padzina la Ambuye ndilo tanthauzo la Mkhristu.

Paulo katatu konse anafuna Ambuye amuchotsere munga, ndipo Ambuye anamva kulira kwake ndipo anamuyankha.

Stefano “Amaitanira ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.”

Khristu ndiye Adonai wa Chipangano Chakale, monga ku Yesaya 6 ndi Yohane 12 komanso Masalmo 110 ndi malo ena otere.

Wokhala pa mpando wachifumu komanso Mwanawankhosa zikulumikizidwa ku Chivumbulutso 5:13; zoonadi pakhoza kukhala funso ngati mutu 4 sungakhale Mwana mu umunthu wake wa umulungu.

‘…Munthu amene anakana kulambira Khristu, komanso sanapeze unkhalapakati wa Iye mbali zonse, sindingathe kuyenda naye. Komatu ndikuganiza kuti kulambira Atate ndi kulambira Khristu monga mkhalapakati zili nawo machitidwe osiyana …’

PEMPHERO KWA KHRISTU MU NYIMBO



Nyimbo zambiri zimaonetsera pemphero, mayamiko ndi malambiro kwa Mwana wa Mulungu wodalitsika.

Zitsanzo zotsatirazi zitionetsera momwe mitima ya iwo olemba nyimbo imalunjika mwachindunji kwa Ambuye Yesu chimodzimodzinso kwa Atate.



Tasonkhana padzina lanu, Ambuye Yesu



Kusiya zonse ndi kuyang’ana kwa Inu,

Kupezeka kwanu kumatipatsa ife chimwemwe,

Muitanira mitima yathu kwa Inu!

Komabe mwa ulemu tikhalabe

Mu mthunzi wa mtanda wanu,

Umene watseka mitima yathu kwamuyaya

Kudziko lapansi ndi nyansi zake zonse.

Mai C A Wellesley, zaka za m’ma 19 Century

Yesu, lingaliro lanu lokhalo

Ndi kukoma kodzala pa chifuwa;

Koma kutitalikira kukoma kukaona nkhope yanu

Komanso mu mpumulo wa kupezeka kwanu.

Bernard wa ku Clairvaux, zaka za m’ma 12 Century



KUMALIDZITSA



Mu phunziro limeneli lokhudza pemphero ndi kulambira kupita kwa Ambuye Yesu, taona zitsanzo khumi ndi chimodzi kuchokera m’Chipangano Chatsopano kuonetsera kuti pemphero likuyenera kuperekedwa kwa Mwana wa Mulungu wodalitsika.

Zikhoza kukhalapo zochuluka.

Kuonjezera apa, taonanso zitsanzo kuchokera mu zolembedwa za mbiri, komanso chitsanzo cha nyimbo mazana mazana zimene zimaimbidwira kwa Ambuye Yesu, kuonetsera kuti pemphero ndi mayamiko (osati mapemphero ndi matamando a mseri okha komanso a pagulu)

Ambuye Yesu atisunge mwa Iye yekha pamene tikufuna kubereka umboni wa gulu kudzina lake lokondedwa ndi kuitanira pa Iye ndi mitima ya ngwiro.

UMBONI WA MUNTHU

Monga Mkhristu watsopano, ndinasonkhanako nawo mu umodzi ya mipingo yodziwika.

Kumeneko ndinauzidwa kuti pali njira imodzi yokha ya kupemphera.

Pemphero la Ambuye2 limene limadziwika kuti ‘pemphero la makono’, ndipo pemphero likuyenera kupita kwa Mulungu Atate m’dzina la Mwana wake, Ambuye Yesu Khristu.

Pasanathe nthawi yaitali, ndinapita mchipinda chimene Akhristu anakumana kupemphera ndi kusanthula Baibulo.

Ndinaona kuti m’bale amene anapemphera, samangotchula kokha Mulungu monga Abba, Atate (onani Agal. 4:6), komanso amapemphera kwa Ambuye Yesu.

Kuonjezera apa, ndinaona kuti nyimbo zimene zimaimbidwa komanso chiphunzitso choperekedwa zimapatsidwa ulemu kwambiri kuposa Khristu wokwezedwayo.

Zaka zochuluka zotsatira, Ambuye anatsogolera mapazi anga kuchoka ku machitidwe amene anthu amapatsidwa malo a pamwamba ndi kuyamba kusonkhana mdzina la Ambuye Yesu mwa Mzimu wake ndi iwo amene afuna kuitanira pa Iye ndi mtima wangwiro.

Ambuye wolemekezeka atsogolere onse akuwerenga ndime zochepazi ku kuzizindikiritsa kwakukulu kwa Iye mwini, ndi kumvera mau ake.

Leonard Layne

Kulankhula Ambuye Yesu mu pemphero ndi malambiro

Madera ena sizichitika, mwinanso nthawi zina ndi zoletsedwa kuti munthu apereke malambiro ndi pemphero kwa Ambuye Yesu Khristu.

Zakhala zikukambidwa kuti munthu mnyumba akhoza kulankhula Ambuye Yesu koma osati mu mpingo; amaonjezeranso kuti palibe munthu akhoza kuletsa mzake mnyumba kuchita zimenezi.

Kotero, zimaoneka zofunikira kuwerenga Malemba pa nkhani yofunikira imeneyi.

Palibe chikaiko chilichonse kunena kuti panali anthu amene analambira Ambuye Yesu pamene anali pano padziko lapansi.

Ku Mateyu 2 anzeru a kummawa anachita chomwechi: iwo ‘anagwa pansi namgwadira Iye’ (ndime 11), komanso pali zitsanzo zochuluka zoterezi (onani Mateyu 8:2; 9:18; 14:33; 15:25; Yohane 9:38).



Zikhoza kutsutsidwa kuti zimenezi zinachitika imfa ya pamtanda isanachitike.

Kenako tikuona zitsanzo za ku Mateyu 28:9, 17 ndi Luka 24:52 kumene anthu anamlambira Ambuye Yesu atauka.

Zoonadi, ku Yohane 20 tili ndi kulankhula kopita kwa Ambuye Yesu: ‘Tomasi anayankha nati kwa iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga’ (ndime 28).



Komabe ena sakhutitsidwa kuti ndi koyenera komanso kofunikira kulambira Ambuye Yesu.

Kodi nanga tsopano pakuti anakwera kupita kumwamba? Tiyeni tilole buku la Chivumbulutso liyankhe.

Pa mutu wa 5 timawerenga, ‘………. akulu makumi awiri mphambu anayi (24) zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, ……… ndipo ayimba nyimbo yatsopano ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse ndi manenedwe onse ndi mitundu yonse; ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko’ (ndime 8-10).

Kuonjezerapo, amene amalimbikira kunena kuti unsembe ndi wa Mulungu yekha, ku Chivumbulutso 20:6 timawerenga: ‘adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu…..’

Ngati imeneyi ndiyo ndondomeko ya machitidwe kumwambako, chifukwa chiyani ndondomekoyi ikhale yosayenerera mu mpingo padziko lapansi lero lino?

Kodi pali njira za kalumikizidwe ndi Ambuye Yesu zochitika ndi oyera mtima ake padziko lino lapansi pamene Iye anakwera kupita kumwamba? Inde zilipo ndithu.

Ku Machitidwe 7 timawerenga za Stefano, munthu wodzala ndi Mzimu Woyera (ndime 55), ‘ali kuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga! Ndipo m’mene anagwada pansi, anafuula ndi mau akulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili’ (ndime 59-60).

Nkovuta kuona munthu wodzala ndi Mzimu Woyera kuchita chinthu chimene tsopano lino ndi choletsedwa.

Ku Machitidwe 9 pali kulumikizana pakati pa Hananiya padziko lapansi ndi Ambuye Yesu kumwamba, Ambuye kupereka malingaliro ake ndipo woyera mtima kupempherera malingalirowo.

Ku 2 Akorinto 12:8 mtumwi Paulo anamufunsa Ambuye katatu konse zokhudza munga mthupi mwake imene inaperekedwa.



Komanso, ku 1 Timoteo 1:12, iye anathokoza Khristu Yesu Ambuye wathu.

‘Koma,’ wina akhoza kulankhula, ‘Onsewa ndi mapemphero a munthu payekha.’

Poyankha, mukuyenera kudziwa kuti pali zitsanzo za anthu monga gulu kulankhula Ambuye Yesu.

Ku Machitidwe 1, gulu la anthu linasonkhana mnyumba yosanjikana kupemphera, ‘Inu Ambuye wozindikira mitima ya onse sonyezani mwa awa awiri m’modziyo amene munamsankha’ (ndime 24).

Ku Machitidwe 13, mu mpingo wa ku Antiokeya, timawerenga za iwo amene amatumikira Ambuye (ndime 2).

Anali magulu amene mtumwi akuwalimbikitsa kudzilankhulira ‘okha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo za uzimu, kuyimbira ndi kuyimba m’malimba Ambuye mu mtima mwanu’ (Aef. 5:19. Onaninso Akol. 3:16).

Tikuyenera kutsindika kuti malo onse amene akulankhula zokhudza Ambuye, ndi Ambuye Yesu amene akulankhulidwa chindunji osati Atate.

Zoonadi, ndi zokaikitsa ngati tingalondole kumutchula Atate kuti Ambuye, pakuti, ‘kwa ife kuli Mulungu m’modzi, Atate …….. ndi Ambuye m’modzi Yesu Khristu’ (1 Akor. 8:6).

Kulankhula kotere kukuoneka kuti kumatengera pa kagwiritsidwe ntchito ka AMBUYE m’Chipangano Chakale, Atate asanavumbulutsidwe kukhala Munthu monga Mwana

Tonse tikuphunzira pa nkhani ya pemphero (Luka 11:1) ndipo sicholinga changa kuti ndikhale otsutsa.

Kodi simomwemo kuti machitachita amodzi a Chikhristu ndiko kulimbana kuletsa pemphero ndi malambiro zopita kwa Ambuye Yesu?

Zikuonetsa kuchokera m’buku la Machitidwe kuti kuitanira padzina la Ambuye ndicho chitsindikizo cha Mkhristu.

Pa mutu 9 Hananiya, mu pemphero lake kwa Ambuye, akulankhula za Saulo wa ku Tariso wakukhala ‘nawo ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lake’ (ndime 14).

Ndipo mu ndime 21 ena amafunsa, ‘suyu iye amene anaononga m’Yerusalemu onse akuitana padzina ili……..’ Zoonadi, kodi munthu amene sanaitanire padzina la Ambuye amapulumutsidwa? (onani Machitidwe 2:21 ndi Aroma 10:13).

Kodi tidzapulumuka bwanji ngati sitiitanira pa dzina la Ambuye?

Kuchokera ku 1 Akorinto 1:2 zikuonetsa kuti ndi chinthu cholondola kwa Akhristu kulankhula Ambuye Yesu:

‘Kwa mpingo wa Mulungu wakukhala m’Korinto ….. ndi onse akuitana padzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.’

Kapena kuti, tsopano zinthu zasokonekera: ‘pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera’ (2 Tim. 2:22)

Munthu kuti apulumutsidwe akuyenera kuitanira kamodzi kokha, kufanizira kwa kuitanira pa dzina la Ambuye ndi gulu la Akhristu ndi kopitilira ndipo pakhale lingaliro kuti oyera mtima aitanire pa Ambuye.

Kulingana ndi kuitanira padzina la Ambuye, zionekera bwino lomwe mowirikiza kuchokera m’Malemba amene akuperekedwa, zina mwa izo, ndi lingaliro la:

  • Kulemekeza umulungu wake ndi mphamvu zake (onani 1 Maf. 18:24; 2 Maf. 5:11);



  • Kudzipereka ku ulamuliro wake ndi kudziwa za ufulu wake (onani Yer. 10:25);

  • Kuitanira kwa Iye kupempha thandizo ndi chiyembekezo cha kuyankhidwa (1 Maf. 18; 2 Maf. 5; Mas. 99:6; Zek. 13:9);

  • Kufika kwa Iye ndi malemekezo komanso mayamiko (Mas. 116:17);

Zingathe kufanizidwa ndi malo amene Iye amakhalako (onani Yer. 3:17)

Zimenezi zinali ku Yerusalemu, monganso zidzakhala mtsogolo, koma lero tikuona machitidwe a chisomo chimene chikuchokera ku ‘Yerusalemu …….. kumwamba’ (Agal. 4:26).

Chomwecho, timasonkhana m’dzina la Ambuye, kuchita m’malo mwa Ambuye pamene Iye palibepo, kuitanira kupezeka kwake, kumpatsa Iye malemekezo ndi matamando athu pamene tinyema mkate pakukumbukira Iye, komanso kufunafuna lingaliro lake ndi mdalitso wake.

Tikuyenera kutsindika kuti zimenezi sizikuletsa pemphero ndi malambiro kupita kwa Mulungu Atate.

Zofunika mu pemphero zikuyenera kugwirizana ndi kumene pempherolo likupita.

Mwa chitsanzo, Ambuye Yesu anatipatsa ife utumiki wa kulalikira uthenga, chomwecho monga mtumiki wa Ambuye, ndikuyenera kufunsa chitsogozo kuchokera kwa Iye zokhudza chimenechi.

Mulungu ndi amene amafunitsitsa kuti anthu onse apulumutsidwe chomwecho mapemphero athu onse a osokera akuyenera kuperekedwa kwa Mulungu (1 Timoteo 2:3-4).

Ndipo monga ana a Mulungu, tikuyenera kulankhula Atate.

Pokhudzana ndi Mgonero wa Ambuye, ndi koyenera kuti tilankhule kwa Ambuye Yesu, pakuti timanyema mkate pokumbukira Iye.

Chimenechi ndi chisonyezo cha mpingo kwa Khristu amene anakonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.

Monga Ambuye ali pakati kutsogolera matamando a Iye yekha kwa Atate (Ahebri. 2:12), Mulungu amapembedzedwa molingana ndi njira imene Iye wakonza kudzionetsera yekha mwa Umunthu wa Mwana wake (Yohane 4:23-24).

Zosangalatsa kuti thunthu lonse la Malemba likumaliza ndi pemphero kwa Ambuye: ‘Idzani Ambuye Yesu’ (Chiv. 22:20).

Wokhulupilira aliyense akuyenera kupemphera pemphero limeneli tsiku ndi tsiku ndipo likhale ndi tanthauzo.

Kodi sichoncho kuti Ambuye Yesu, mwakulankhula kwa Iye yekha padziko lino lapansi, afunitsitsa ubale wa banja mu mpingo; kuti ake omwe afunitsitse kupezeka kwake kwenikweni monganso Iye afunitsitsa iwo kukhala naye? ‘Mzimu ndi mkwatibwi anene, idzani’ (Chiv. 22:17).

Mark Best